Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  August 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 110-118

‘Kodi Yehova Ndidzamubwezera Chiyani?’

‘Kodi Yehova Ndidzamubwezera Chiyani?’

Munthu amene analemba Masalimo amenewa ankaona kuti Yehova wamuchitira zazikulu pomupulumutsa ku “zingwe za imfa.” (Sal. 116:3) Iye anatsimikiza mtima kumuthokoza Yehova poyesetsa kuchita zonse zimene Mulunguyo amafuna komanso kukwaniritsa zinthu zonse zimene anamulonjeza.

Kodi ndi zinthu zotani zimene Yehova wandichitira mlungu uno?

Kodi ndingamuthokoze bwanji Yehova chifukwa cha zomwe wandichitira?