Davide akamafotokoza zokhudza kukoma mtima kwa Yehova, ankagwiritsa ntchito mawu oyerekezera.

  • 103:11

    N’zosatheka kudziwa bwinobwino kuti kumwamba n’kotalikirana bwanji ndi dziko lapansi. Mofanana ndi zimenezi n’zovutanso kumvetsa kuti kukoma mtima kwa Yehova kumafika pati

  • 103:12

    Yehova amaika machimo athu kutali kwambiri ndi ife, ngati mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo

  • 103:13

    Mofanana ndi mmene bambo amachitira chifundo mwana wake amene wavulala, nayenso Yehova amachitira chifundo munthu amene akumva chisoni chifukwa cha machimo ake