Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  August 2016

August 1-7

MASALIMO 87-91

August 1-7
 • Nyimbo Na. 49 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Pitirizani Kukhala M’malo Otetezeka a Wam’mwambamwamba”: (10 min.)

  • Sal. 91:1, 2—Timatetezeka mwauzimu tikakhala “m’malo achitetezo” a Yehova (w10 2/15 26-27 ndime 10-11)

  • Sal. 91:3—“Wosaka mbalame” akufunitsitsa kutigwira (w07 10/1 26-30 ndime 1-18)

  • Sal. 91:9-14—Yehova ndi pothawirapo pathu (w10 1/15 10-11 ndime 13-14; w01 11/15 19-20 ndime 13-19)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Sal. 89:34-37—Kodi ndi pangano liti limene lafotokozedwa palembali? Nanga kodi Yehova anagwiritsa ntchito chitsanzo chotani pofuna kusonyeza kuti panganoli ndi lodalirika? (w14 10/15 10 ndime 14; w07 7/15 32 ndime 3-4)

  • Sal. 90:10, 12—Kodi ‘tingawerengere bwanji masiku athu kuti tikhale ndi mtima wanzeru’? (w06 7/15 13 ndime 4; w01 11/15 13 ndime 19)

  • Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 90:1-17

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Nkhani yokambirana. Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyo. Limbikitsani ofalitsa kuti alembe ulaliki wawowawo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU