10:13

Ngakhale kuti Yehova akhoza kutichotsera mayesero, nthawi zambiri amapereka “njira yopulumukira.” Iye amachita zimenezi potipatsa zinthu zofunikira kuti tithe kupirira mayesero omwe takumana nawo.

  • Angatithandize kuti maganizo ndi mtima wathu zikhale m’malo pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake woyera komanso zinthu zauzimu zomwe amatipatsa.​—Mat. 24:45; Yoh. 14:16; Aroma 15:4

  • Akhoza kutitsogolera pogwiritsa ntchito mzimu woyera womwe ungatithandize kukumbukira mfundo komanso zitsanzo za anthu a m’Baibulo. Angatithandizenso kuganizira njira yabwino yomwe tingasankhe.​—Yoh. 14:26

  • Akhozanso kugwiritsa ntchito angelo ake kuti atithandize.​—Aheb. 1:14

  • Angagwiritsenso ntchito abale ndi alongo athu.​—Akol. 4:11