1:3, 4

Njira imodzi imene Yehova amagwiritsa ntchito potitonthoza ndi kugwiritsira ntchito abale ndi alongo athu mumpingo. Kodi tingalimbikitse bwanji Akhristu amene aferedwa?

  • Muziwamvetsera ndipo musamawadule mawu

  • “Lirani ndi anthu amene akulira.”​—Aroma 12:15

  • Mungawalembere khadi, kalata, imelo kapena meseji yowalimbikitsa.​—w17.07 15, bokosi

  • Mukhoza kupemphera nawo limodzi komanso kuwatchula m’mapemphero anu