KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Yehova, yemwe ndi Mlangizi wathu wamkulu, amatipatsa maphunziro apamwamba kwambiri. Amatiphunzitsa kuti tisinthe moyo wathu komanso amatithandiza kuti tidzakhale ndi moyo wabwino m’tsogolo. Iye amachita zimenezi kwaulere. (Yes. 11:6-9; 30:20, 21; Chiv. 22:17) Pogwiritsa ntchito maphunziro amenewa, Yehova amatithandiza kuti tikhale okonzeka kuuza ena uthenga umene ungawathandize kuti adzapulumuke.​—2 Akor. 3:5.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Tiyenera kukhala odzichepetsa komanso ofatsa.​—Sal. 25:8, 9

  • Muzigwiritsa ntchito mwayi wamaphunziro umene muli nawo panopa, mwachitsanzo mukapatsidwa nkhani za ophunzira mumsonkhano wamkati mwa mlungu, muziyesetsa kuzikamba bwino

  • Khalani ndi zolinga zauzimu zomwe mungazikwaniritse.​—Afil. 3:13

  • Sinthani zinthu zina ndi zina kuti mupitirize kuphunzitsidwa ndi Yehova.​—Afilipi 3:8

ONERANI VIDIYO YAKUTI TINAPEZA MADALITSO AMBIRI CHIFUKWA CHOPHUNZITSIDWA NDI YEHOVA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ofalitsa ena alimbana ndi mavuto otani kuti akwanitse kulowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?

  • Kodi anthu amaphunzira zotani akalowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?

  • Kodi abale ndi alongo anathandiza bwanji Akhristu omwe anatumizidwa mumpingo wawo atamaliza maphunziro awo?

  • Kodi Mkhristu ayenera kukwaniritsa zinthu ziti kuti alowe nawo mu Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu? (kr 189)

  • Kodi ndi masukulu ena ati omwe mungalowe m’gulu la Yehova?

Kodi mungapeze madalitso otani ngati mutalola kuti Yehova akuphunzitseni?