CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Kusakhala Pabanja ndi Mphatso”: (10 min.)

  • 1 Akor. 7:32​—Akhristu omwe sali pabanja amatumikira Yehova popanda kuda nkhawa ndi mavuto amene anthu apabanja amakumana nawo (w11 1/15 18 ¶3)

  • 1 Akor. 7:33, 34​—Akhristu omwe ali pabanja “amadera nkhawa zinthu za dziko” (w08 7/15 27 ¶1)

  • 1 Akor. 7:37, 38​—Akhristu omwe asankha kusakhala pabanja n’cholinga choti achite zambiri potumikira Yehova ‘amachita bwino koposa’ amene ali pabanja (w96 10/15 12-13 ¶14)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • 1 Akor. 7:11​—Kodi n’chiyani chingachititse Mkhristu kusankha kuti apatukane ndi mwamuna kapena mkazi wake? (lvs 251)

  • 1 Akor. 7:36​—N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kulowa m’banja ‘akapitirira pachimake pa unyamata’? (w00 7/15 31 ¶2)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) 1 Akor. 8:1-13 (th phunziro 5)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 37

 • Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi Yomwe Simuli Pabanja: (15 min.) Onerani vidiyoyi. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi Akhristu amene sali pabanja amakumana ndi mavuto otani? (1 Akor. 7:39) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mwana wa Yefita ndi chitsanzo chabwino? Kodi Yehova amadalitsa bwanji anthu amene amakhalabe okhulupirika? (Sal. 84:11) Kodi abale ndi alongo mumpingo angalimbikitse bwanji Akhristu omwe sali pabanja? Kodi Akhristu omwe sali pabanja ali ndi mwayi wochita mautumiki ati?

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 32

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 117 ndi Pemphero