CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Kodi Tingamvere Bwanji Lamulo Lakuti, Pitani Mukaphunzitse Anthu?”: (10 min.)

  • Mat. 28:18​—Yesu ali ndi ulamuliro waukulu (w04 7/1 8 ¶4)

  • Mat. 28:19​—Yesu anayambitsa ntchito yapadziko lonse yolalikira komanso kuphunzitsa (“mukaphunzitse” “anthu a mitundu yonse” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 28:19, nwtsty)

  • Mat. 28:20​—Tiyenera kuphunzitsa anthu komanso kuwathandiza kuti azitsatira zonse zimene Yesu anaphunzitsa (“ndi kuwaphunzitsa” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 28:20, nwtsty)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Mat. 27:51​—Kodi kung’ambika pakati kwa nsalu yotchinga kunkaimira chiyani? (“nsalu yotchinga” “m’nyumba yopatulika” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 27:51, nwtsty)

  • Mat. 28:7​—Kodi mngelo wa Yehova anasonyeza bwanji kuti analemekeza azimayi omwe anapita kumanda a Yesu? (“mukauze ophunzira ake kuti wauka” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 28:7, nwtsty)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mat. 27:38-54

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene.

 • Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Woyamba: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.

 • Nkhani: (Osapitirira 6 min.) g17.2 14​—Mutu: Kodi Yesu Anafera Pamtanda?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU