Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  April 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za Ulaliki

GALAMUKANI!

Funso: Masiku ano, mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV amakonda kuonetsa zamatsenga monga zokhudza ufiti, mizukwa ndi zina. Kodi mumaona kuti pali vuto lililonse kuonera zinthu zimenezi?

Perekani Magaziniyo: Galamukani! iyi ikufotokoza chifukwa chimene anthu ena amachitira chidwi ndi nkhani zamatsenga komanso zoona zake za nkhaniyi.

KUPHUNZITSA CHOONADI

Funso: Kodi Ufumu wa Mulungu udzathetsa bwanji mavuto padzikoli?

Lemba: Mat. 6:10

Zoona Zake: Ufumu wa Mulungu udzabweretsa mtendere, mgwirizano komanso chitetezo padzikoli ngati mmene zilili kumwamba.

KODI UFUMU WA MULUNGU N’CHIYANI? (Ulendo wobwereza)

Funso: [Musonyezeni funso limene mudzakambirane pa ulendo wotsatira lomwe lili kuseri kwa kapepalaka.] Kodi moyo udzakhala wotani mu Ufumu wa Mulungu?

Malemba: Sal. 37:29; Yes. 65:21-23

Perekani Kabuku: [Musonyezeni kabuku ka Uthenga Wabwino.] Phunziro 7 m’kabukuka likufotokoza mmene anthufe tidzapindulire malonjezo amenewa akadzakwaniritsidwa. [Yambitsani phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito kabukuka.]

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.