Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 25-28

Khalani Olimba Mtima Ngati Yeremiya

Khalani Olimba Mtima Ngati Yeremiya

Yeremiya anachenjeza kuti Yerusalemu adzawonongedwa ngati mmene anawonongedwera Silo

26:6

  • Pa nthawi ina, likasa la pangano lomwe linali umboni woti Yehova ankatsogolera anthu ake, linkasungidwa ku Silo

  • Yehova analola kuti Afilisiti akalande likasalo ndipo silinabwererenso ku Silo

Ansembe, aneneri ndi anthu onse ankafuna kupha Yeremiya

26:8, 9, 12, 13

  • Anthu anagwira Yeremiya chifukwa ankanena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi

  • Yeremiya sanathawe kapena kusiya kutumikira Mulungu

Yehova anateteza Yeremiya

26:16, 24

  • Yeremiya anapitiriza kukhala wolimba mtima ndipo Yehova sanamusiye

  • Mulungu anachititsa kuti Ahikamu, yemwe anali wolimba mtima, ateteze Yeremiya

Yeremiya analengeza uthenga kwa zaka 40 ngakhale kuti anthu ambiri sankasangalala nawo. Iye anakwanitsa zimenezi chifukwa choti yehova ankamulimbikitsa komanso kumuthandiza