Kodi ndi ndani omwe tiyenera kuwalandira ndi manja awiriwa? Ndi aliyense amene amabwera kumisonkhano yathu. (Aroma 15:7; Aheb. 13:2) Angakhale atsopano, Mkhristu mnzathu yemwe wachokera kudziko lina kapenanso Mkhristu amene anasiya kusonkhana kwa nthawi yaitali. Taganizirani muli inuyo, kodi simungathokoze ena atakulandirani ndi manja awiri? (Mat. 7:12) Choncho, bwanji osayesa kuchita khama kuti muzipereka moni mu Nyumba ya Ufumu, misonkhano isanayambe komanso ikatha? Izi zimathandiza kuti onse mumpingo azikondana ndiponso Yehova amalemekezedwa. (Mat. 5:16) N’zoona kuti sizingatheke kulankhulana ndi aliyense. Komabe tikamayesetsa, aliyense amaona kuti walandiridwa. *

Tiyenera kulandira bwino anthu nthawi zonse osati pa nthawi ya Chikumbutso yokha. Atsopano akaona chikondi pakati pathu, amalemekeza Mulungu ndipo zimawalimbikitsa kuti ayambe kulambira nafe limodzi.​—Yoh. 13:35.

^ ndime 3 Tiyenera kukumbukira kuti Baibulo limaletsa kulankhulana ndi anthu ochotsedwa kapena odzilekanitsa.​—1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10.