Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mungathe Kulimbikitsa Mkhristu Amene Anafooka

Mungathe Kulimbikitsa Mkhristu Amene Anafooka

Chaka chilichonse, ena mwa amene amapezeka pa Chikumbutso ndi Akhristu omwe anafooka. Akhristuwa anayamba kuthamanga nawo pampikisano wa moyo koma anafooka pa zifukwa zosiyanasiyana. Zina mwa zifukwazi zafotokozedwa m’kabuku kakuti Bwererani kwa Yehova. (Aheb. 12:1) Komabe, Yehova yemwe anawagula ndi magazi a Mwana wake, amaona kuti Akhristu amenewa ndi amtengo wapatali. (Mac. 20:28; 1 Pet. 1:18, 19) Ndiye kodi tingawathandize bwanji kuti abwererenso mumpingo?

Mofanana ndi m’busa amene amayesetsa kufunafuna nkhosa imene yasochera, akulu amafufuza komanso kuthandiza anthu amene anafooka. (Luka 15:4-7) Izi zimasonyeza chikondi cha Yehova. (Yer. 23:3, 4) Tonsefe osati akulu okha, tingathe kulimbikitsa anthu oterewa. Yehova amasangalala tikamakomera mtima komanso kusonyeza chikondi anthu amene anafooka ndipo amatidalitsa. (Miy. 19:17; Mac. 20:35) Choncho tingachite bwino kuganizira munthu woti timulimbikitse ndipo tiyenera kuchita zimenezi mwamsanga.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZILIMBIKITSA AMENE ANAFOOKA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Abbey anachita chiyani atakumana ndi wa Mboni amene sankamudziwa?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwitsa akulu tisanayambe kuthandiza munthu amene anafooka?

  • Kodi Abbey anakonzekera zinthu ziti paulendo wake wachiwiri wokakumana ndi Laura?

  • Kodi Abbey anasonyeza bwanji kupirira, kuleza mtima komanso chikondi pamene ankathandiza Laura?

  • Kodi tikuphunzira chiyani mu fanizo la Yesu lopezeka pa Luka 15:8-10?

  • Kodi panakhala zotsatira zotani chifukwa cha khama limene linalipo pothandiza Laura