Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mlongo amene anafooka walandiridwanso kumpingo

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU April 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za ulaliki wa Galamukani! ndiponso kuphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Muzilola Kuti Yehova Aziumba Maganizo ndi Makhalidwe Anu

Woumba Wamkulu amatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino, koma ifenso tiyenera kuchita mbali yathu.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muziwalandira ndi Manja Awiri

Aliyense akabwera kumisonkhano yathu, aziona kuti timakondana. Kodi tingathandize bwanji kuti anthu akafika pa Nyumba ya Ufumu aziona kuti alandiridwa?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kodi Muli ndi “Mtima Wodziwa” Yehova?

Mu Yeremiya chaputala 24, Yehova anayerekezera anthu ndi nkhuyu. Kodi ndi ndani amene anali ngati nkhuyu zabwino, ndipo tingawatsanzire bwanji masiku ano?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mungathe Kulimbikitsa Mkhristu Amene Anafooka

Yehova amaona kuti Akhristu amene anafooka ndi amtengo wapatali. Ndiye kodi tingawathandize bwanji kuti abwererenso mumpingo?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Khalani Olimba Mtima Ngati Yeremiya

Yeremiya ankalengeza kuti Yerusalemu awonongedwa. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti akhale wolimba mtima?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Nyimbo za Ufumu Zimatithandiza Kukhala Olimba Mtima

Kuimba nyimbo za Ufumu kunalimbikitsa Akhristu amene anali mundende ya ku Sachsenhausen. Nafenso tikakumana ndi mavuto nyimbo zingatilimbikitse.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Ananeneratu za Pangano Latsopano

Kodi pangano latsopano ndi losiyana bwanji ndi pangano la Chilamulo, nanga pangano latsopanoli lidzapindulitsa bwanji anthu kwamuyaya?