GALAMUKANI!

Perekani Magaziniyo: Ndikufuna ndikupatseni magazini yatsopano iyi ya Galamukani!

Funso: Taonani funso lomwe lili patsamba 2. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Lemba: Luka 7:35

Nkhani imeneyi ikufotokoza mmene tingapindulire ndi mfundo za m’Baibulo.

GALAMUKANI!

Funso: Kodi nanunso mumaona kuti kutsatira mfundo ya palemba ili n’kothandiza?

Lemba: Mat. 6:34

Perekani Magaziniyo: [Tsegulani nkhani yakuti, “Zimene Baibulo Limanena—Nkhawa.”] Nkhaniyi ikufotokoza mmene Baibulo lingatithandizire tikakhala ndi nkhawa.

Baibulo Limaphunzitsa Chiyani

Funso: Anthu ambiri amene amakhulupirira Mulungu, amafunitsitsa kumudziwa bwino. Kodi mukudziwa kuti Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyandikire Mulungu?

Lemba: Yak. 4:8a

Perekani Bukulo: Buku ili linalembedwa n’cholinga chotithandiza kuphunzira za Mulungu pogwiritsa ntchito Baibulo. [Sonyezani mutu woyamba wa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.]

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.