Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zofunika Kukumbukira Pamsonkhano Wachigawo

Zofunika Kukumbukira Pamsonkhano Wachigawo

Pa nthawi ya msonkhano wachigawo tikufunitsitsa kudzasonyeza anthu chikondi ngati mmene timachitira nthawi zonse. (Mateyu 22:37-39) Lemba la 1 Akorinto 13:4-8, limafotokoza zimene chikondi chimachita, limati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. . . . sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. . . . Chikondi sichitha.” Mukamaonera vidiyo ya Zofunika Kukumbukira Pamsonkhano Wachigawo, muziganizira mmene mungadzasonyezere ena chikondi pa nthawi ya msonkhano.

KODI TINGASONYEZE BWANJI CHIKONDI . . .

  • tikamasunga malo okhala?

  • nyimbo zomvetsera zikatsala pang’ono kuyamba?

  • kumalo ogona ngati tapeza malo kuhotelo kapenanso kwinakwake?

  • tikamadzipereka kugwira nawo ntchito zina?