Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  April 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 33-37

Mnzako Weniweni Amakuuza Malangizo Othandiza

Mnzako Weniweni Amakuuza Malangizo Othandiza
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

Elihu atayamba kuyankhula, ananena malangizo abwino kwambiri kusiyana ndi amene ananena Elifazi, Bilidadi ndi Zofari. Ankachitanso zinthu mokoma mtima pa nthawi imene ankayankhula ndi Yobu. Zimene anachitazi zikusonyeza kuti anali mnzake weniweni wa Yobu amene anamuthandizadi. Ndipo ife tingachite bwino kumutsanzira.

MLANGIZI WABWINO AYENERA KUKHALA:

ELIHU NDI CHITSANZO CHABWINO

32:4-7, 11, 12; 33:1

 

 • WOLEZA MTIMA

 • WOMVETSERA

 • WAULEMU

 
 • Elihu anadikira moleza mtima kuti anzake a Yobu omwe anali aakulu kwa iyeyo amalize kaye kuyankhula

 • Iye anamvetsera kaye nkhaniyo mwatcheru n’cholinga choti amupatse Yobu malangizo othandiza

 • Poyankhula ndi Yobu ankamutchula dzina lake komanso ankamuyankhula monga mnzake wapamtima

 

33:6, 7, 32

 

 • WODZICHEPETSA

 • WOCHEZEKA

 • WACHIFUNDO

 
 • Elihu anali wodzichepetsa komanso wokoma mtima ndipo anavomereza kuti nayenso anabadwa ndi uchimo

 • Ankamumvera chifundo Yobu chifukwa cha mavuto ake

 

33:24, 25; 35:2, 5

 

 • WOGANIZA BWINO

 • WOKOMA MTIMA

 • WOOPA MULUNGU

 
 • Elihu anathandiza Yobu kuzindikira kuti ankaganiza molakwika

 • Elihu anathandiza Yobu kuti asamaone ngati chinthu chofunika kwambiri ndicho kudziona ngati wolungama

 • Malangizo a Elihu anathandiza kwambiri kuti Yobu asavutike kulandira malangizo ochokera kwa Yehova