Satana amanena zinthu zabodza pofuna kufooketsa atumiki a Yehova masiku ano. Taonani mfundo zopezeka m’buku la Yobu, zosonyeza kusiyana pakati pa mabodza a Satana ndi mmene Yehova amawonera atumiki ake. Lembani mavesi ena amene amakutsimikizirani kuti Yehova amakuganizirani.

MABODZA OMWE SATANA AMANENA

MMENE YEHOVA AMAONERA ATUMIKI AKE

Mulungu ali ndi mfundo zokhwima ndipo amaona kuti palibe chanzeru chimene atumiki ake angachite. Zolengedwa zake zonse sizingamusangalatse (Yobu 4:18; 25:5)

Yehova amayamikira kwambiri tikamayesetsa kumutumikira modzichepetsa (Yobu 36:5)

Munthu ndi wosafunika kwa Mulungu (Yobu 22:2)

Yehova amasangalala ndiponso amatidalitsa tikamamutumikira mokhulupirika (Yobu 33:26; 36:11)

Mulungu alibe nazo kanthu kuti ndiwe wolungama (Yobu 22:3)

Yehova amasamalira olungama (Yobu 36:7)