Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  April 2016

April 11-17

YOBU 21-27

April 11-17
 • Nyimbo Na. 83

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Yobu Sanalole Kuti Maganizo Olakwika Amusokoneze”: (10 min.)

  • Yobu 22:2-7—Elifazi anapatsa Yobu malangizo popanda umboni woti analidi wolakwa (w06 3/15 15 ndime 6; w05 9/15 26-27; w95 2/15 27 ndime 6))

  • Yobu 25:4, 5—Bilidadi anauza Yobu maganizo olakwika (w05 9/15 26-27)

  • Yobu 27:5, 6—Yobu sanalole kuti zonena za ena zimuchititse kudziona ngati walephera kukhala ndi mtima wosagawanika (w09 8/15 4 ndime 8; w06 3/15 15 ndime 8)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Yobu 24:2—Kodi n’chifukwa chiyani munthu yemwe wasuntha malire a mnzake ankaonedwa kuti wapalamula mlandu waukulu? (it-1-E 360)

  • Yobu 26:7—Kodi ndi mfundo iti yochititsa chidwi imene Yobu ananena yokhudza mmene dziko liliri? (w15 6/1 5 ndime 4; w11 7/1 26 ndime 2-5)

  • Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: Yobu 27:1-23 (Osapitirira 4 min.)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 129

 • Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani?: (15 min.) Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuonetsa vidiyo ya pawebusaiti yathu ya jw.org/ny yakuti, Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani? (Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA.) Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi munthu angavutitsidwe pazifukwa ziti? Kodi munthu yemwe amavutitsidwa angakumane ndi mavuto ati? Kodi mungatani ngati anzanu amakuvutitsani kapenanso kuti asamakuvutitseni? Kodi mungauze ndani ngati wina akukuvutitsani? Pomaliza fotokozani mfundo za m’buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amadzifunsa, Buku Lachiwiri mutu 14.

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: cl mutu 28 ndime 18-21 ndi bokosi patsamba 289 (30 min.)

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 23 ndi Pemphero