Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Zekariya 9:1-17

9  Uthenga+ wokhudza dziko la Hadiraki: “Awa ndi mawu a Yehova oweruza dziko la Hadiraki, ndipo akuweruzanso Damasiko.+ Pakuti maso a Yehova akuyang’ana anthu+ komanso mafuko onse a Isiraeli.  Mawu amenewa akuweruzanso Hamati+ amene anachita naye malire. Komanso akuweruza Turo+ ndi Sidoni+ chifukwa ali ndi nzeru zambiri.+  Turo anamanga chiunda chomenyerapo nkhondo.* Anadziunjikira siliva wochuluka ngati dothi ndiponso golide wochuluka ngati matope a m’misewu.+  Yehova adzamulanda chuma chake ndipo gulu lake lankhondo adzaliphera m’nyanja.+ Koma iye adzatenthedwa ndi moto.+  Asikeloni adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha. Gaza adzamva ululu waukulu. Izi zidzachitikiranso Ekironi+ chifukwa chakuti amene anali kumudalira+ adzachita manyazi. Ku Gaza sikudzakhalanso mfumu ndipo m’dziko la Asikeloni simudzakhalanso anthu.+  Mwana wochokera mu mtundu wina wa anthu+ adzakhala mu Asidodi,+ ndipo ine ndidzathetsa kunyada kwa Afilisiti.+  Ndidzachotsa zinthu zake zamagazi m’kamwa mwake ndipo ndidzachotsa chakudya chake chonyansa pakati pa mano ake.+ Aliyense amene adzatsale adzakhala wa Mulungu wathu. Wotsalayo adzakhala ngati mfumu+ mu Yuda,+ ndipo Ekironi adzakhala ngati Myebusi.+  Ndidzamanga msasa kunja kwa nyumba yanga kuti ndizidzailondera,+ moti sipadzakhalanso munthu wolowa kapena kutuluka. Kapitawo sadzadutsanso pakati pawo+ pakuti ine ndaona ndi maso anga zimene zinawachitikira.+  “Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni sangalala kwambiri.+ Fuula mokondwera+ iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu. Taona, mfumu yako+ ikubwera kwa iwe.+ Mfumuyo ndi yolungama ndipo yapambana.+ Iyo ndi yodzichepetsa+ ndipo ikubwera itakwera bulu. Ikubwera itakwera nyama yokhwima, imene ndi mwana wamphongo wa bulu.+ 10  Ndidzawononga magaleta ankhondo mu Efuraimu ndiponso mahatchi mu Yerusalemu.+ Mauta omenyera nkhondo+ adzathyoledwa. Mfumuyo idzalankhula mawu amtendere kwa anthu a mitundu ina.+ Ulamuliro wake udzayambira kunyanja mpaka kukafika kunyanja. Ndiponso udzachokera ku Mtsinje* mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+ 11  “Koma mkazi iwe, chifukwa cha magazi a pangano limene unapangana ndi ine,+ ndidzatulutsa akaidi ako+ m’dzenje lopanda madzi. 12  “Inu akaidi amene muli ndi chiyembekezo,+ bwererani kumalo a chitetezo champhamvu.+ “Komanso, ine lero ndikunena kuti, ‘Mkazi iwe, ndidzakupatsa magawo awiri a madalitso.+ 13  Yuda ndidzamupinda kuti akhale uta wanga. Efuraimu ndidzamuika pa uta umenewo ngati muvi. Iwe Ziyoni, ine ndidzadzutsa ana ako+ kuti aukire ana a Girisi.+ Ndipo ndidzakusandutsa lupanga la munthu wamphamvu.’+ 14  Zidzakhala zoonekeratu kuti Yehova ali ndi anthu ake,+ ndipo muvi wake udzathamanga ngati mphezi.+ Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa adzaliza lipenga lanyanga ya nkhosa,+ ndipo adzapita ndi mphepo yamkuntho ya kum’mwera.+ 15  Yehova wa makamu adzatchinjiriza anthu ake. Adani awo adzawalasa ndi miyala yoponya ndi gulaye* koma iwo adzagonjetsa adaniwo.+ Iwo adzasangalala ndipo adzafuula ngati amwa vinyo.+ Adzadzazidwa ngati mbale zolowa ndiponso ngati mmene magazi amadzazira m’makona a guwa lansembe.+ 16  “Pa tsiku limenelo, Yehova Mulungu adzapulumutsa nkhosa zake,+ zimene ndi anthu ake.+ Pakuti iwo adzakhala ngati miyala yonyezimira ya pachisoti chachifumu m’dziko lake.+ 17  Ubwino wake ndi waukulu kwambiri+ ndiponso iye ndi wooneka bwino kwambiri.+ Tirigu adzapatsa mphamvu anyamata ndipo vinyo watsopano adzapatsa mphamvu anamwali.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala ndi dzanja chimene amachita kupukusa. M’madera ena amati mvuluma kapena ulaya.