Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zekariya 8:1-23

8  Yehova wa makamu anapitiriza kulankhula kuti:  “Yehova wa makamu+ wanena kuti: ‘Ziyoni ndidzam’chitira nsanje kwambiri.+ Ndidzam’chitira nsanje ndi kukwiya kwambiri.’”+  “Yehova wanena kuti, ‘Ndidzabwerera ku Ziyoni+ ndipo ndidzakhala mu Yerusalemu.+ Yerusalemu adzatchedwadi mzinda wa choonadi+ ndi phiri loyera+ la Yehova+ wa makamu.’”  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘M’bwalo la mzinda wa Yerusalemu mudzakhala amuna ndi akazi achikulire.+ Aliyense adzatenga ndodo+ m’dzanja lake pakuti masiku ake adzakhala atachuluka.  M’mabwalo a mzindawo mudzadzaza anyamata ndi atsikana ndipo azidzasewera mmenemo.’”+  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ngakhale kuti m’masiku amenewo otsalira a anthu awa adzaona kuti zimenezo n’zosatheka, kodi zidzakhalanso zosatheka kwa ine?’+ watero Yehova wa makamu.”  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndipulumutsa anthu anga kuchokera kudziko la kum’mawa ndiponso kuchokera kudziko la kumadzulo.+  Ndithu ndidzawabweretsa, ndipo adzakhala mu Yerusalemu.+ Iwo adzakhala anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo woona ndi wachilungamo.’”+  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Limbani mtima anthu inu ndipo mukonzeke kugwira ntchito,+ inu amene mukumva mawu a aneneri masiku ano.+ Awa ndi mawu amene aneneriwo ananena pa tsiku limene maziko a nyumba ya Yehova wa makamu anayalidwa kuti kachisi amangidwe.+ 10  Masiku amenewo asanafike, anthu ndi ziweto sanali kulandira malipiro.+ Munthu wa pa ulendo, adani anali kumusowetsa mtendere,+ chifukwa ine ndinali kuyambanitsa anthu onse.’+ 11  “‘Anthu anga otsala sindidzawachitiranso zinthu ngati zimene ndinawachitira masiku akale,’+ watero Yehova wa makamu. 12  ‘M’dzikolo mudzakhala mbewu ya mtendere.+ Mpesa udzabala zipatso+ ndipo dziko lapansi lidzapereka zokolola zake.+ Kumwamba kudzagwetsa mame ake.+ Ndidzachititsa kuti anthu otsala+ mwa anthu awa adzalandire zinthu zonsezi.+ 13  Monga mmene munakhalira temberero pakati pa anthu a mitundu ina,+ inu a nyumba ya Yuda ndi a nyumba ya Isiraeli,+ ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala dalitso.+ Musachite mantha.+ Limbani mtima ndipo mukonzeke kugwira ntchito.’+ 14  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘“Monga mmene ndinatsimikizira mtima kuchitapo kanthu pamene ndinakugwetserani tsoka chifukwa chakuti makolo anu anandikwiyitsa,+ ndipo sindinakumvereni chisoni,”+ watero Yehova wa makamu, 15  “tsopano ndatsimikizanso mtima kuchitapo kanthu, koma ulendo uno ndichitira zabwino Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda.+ Choncho musachite mantha.”’+ 16  “‘Anthu inu muzichita zinthu izi:+ Muzilankhulana zoona zokhazokha.+ Poweruza milandu m’zipata za mizinda yanu, muziweruza mogwirizana ndi choonadi komanso molimbikitsa mtendere.+ 17  Musamakonzerane ziwembu mumtima mwanu kuti muonetsane tsoka+ ndipo musamakonde kulumbira monama.+ Pakuti zinthu zonsezi ine ndimadana nazo,’+ watero Yehova.” 18  Yehova wa makamu anapitiriza kundiuza kuti: 19  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Kusala kudya kwa m’mwezi wachinayi,+ kusala kudya kwa m’mwezi wachisanu,+ kusala kudya kwa m’mwezi wa 7+ ndiponso kusala kudya kwa m’mwezi wa 10,+ kudzakhala kusala kudya kosangalatsa ndi kokondweretsa kwa nyumba ya Yuda. Komanso nthawi za kusala kudya zimenezi zidzakhala nyengo zabwino zazikondwerero.+ Choncho muzikonda choonadi ndi kulimbikitsa mtendere.’+ 20  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ndithu anthu a mitundu ina ndi anthu okhala m’mizinda yambiri adzabwera.+ 21  Anthu okhala mumzinda umodzi adzapita kwa anthu okhala mumzinda wina n’kuwauza kuti: “Tiyeni tipite!+ Tiyeni tipite kukakhazika pansi mtima+ wa Yehova ndi kufunafuna Yehova wa makamu. Inenso ndipita nawo.”+ 22  Anthu ambiri a mitundu ina ndiponso mitundu yamphamvu ya anthu idzabweradi kudzafunafuna Yehova wa makamu mu Yerusalemu.+ Idzabwera kudzakhazika pansi mtima wa Yehova.’ 23  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘M’masiku amenewo, amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina+ adzagwira+ chovala cha munthu amene ndi Myuda+ ndi kunena kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi,+ chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”’”+

Mawu a M'munsi