Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Zekariya 7:1-14

7  M’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo,+ Yehova analankhula ndi Zekariya pa tsiku lachinayi m’mwezi wa 9, umene ndi mwezi wa Kisilevi.+  Anthu a ku Beteli anatumiza Sarezere ndi Regemu-meleki limodzi ndi anthu ake, kuti akakhazike pansi+ mtima wa Yehova.  Anawatuma kuti akauze ansembe+ a panyumba ya Yehova wa makamu ndi aneneri kuti: “Kodi tilire* m’mwezi wachisanu+ ndi kukhala osadya ngati mmene takhala tikuchitira zaka zonsezi?”+  Yehova wa makamu anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Kauze anthu onse a m’dzikoli ndi ansembe kuti, ‘Pamene munali kusala kudya+ ndi kulira m’mwezi wachisanu komanso m’mwezi wa 7+ kwa zaka 70,+ kodi munalidi kusala kudya chifukwa cha ine?+  Pamene munali kudya ndi kumwa, kodi simunali kudya ndi kumwa kuti mudzisangalatse nokha?  Kodi simunayenera kumvera mawu+ amene Yehova ananena kudzera mwa aneneri akale,+ pamene mu Yerusalemu ndi mizinda yake yonse yozungulira munali kukhala anthu, komanso pamene munali bata? Kodi simunayenera kumvera Mulungu pamene ku Negebu+ ndi ku Sefela+ kunali kukhala anthu?’”  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Zekariya kuti:  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Muzichita chilungamo chenicheni poweruza milandu.+ Muzisonyezana kukoma mtima kosatha+ ndi chifundo.+ 10  Musamabere mwachinyengo mkazi wamasiye,+ mwana wamasiye,*+ mlendo+ kapena munthu wosautsika.+ Musamakonzerane chiwembu mumtima mwanu.’+ 11  Koma iwo anakanabe kumvetsera.+ Anapitiriza kumulozetsa nkhongo+ ndipo anatseka makutu awo kuti asamve chilichonse.+ 12  Iwo anaumitsa mtima wawo+ ngati mwala wolimba kwambiri kuti asamvere malamulo+ ndi mawu a Yehova wa makamu, amene anawatumizira mwa mzimu wake+ kudzera mwa aneneri akale.+ Choncho Yehova wa makamu anakwiya kwambiri.”+ 13  “‘Popeza kuti ine ndikawaitana sanali kundimvera,+ iwonso akandiitana sindinali kuwamvera,’+ watero Yehova wa makamu. 14  ‘Chotero ndinawabalalitsira ku mitundu yonse ya anthu+ imene sanali kuidziwa,+ ngati kuti atengedwa ndi mphepo yamkuntho. Dzikoli analisiya labwinja, popanda munthu wodutsamo kapena kuyendayendamo.+ Iwo anasandutsa dziko losiririka+ kukhala chinthu chodabwitsa.’”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ndilire.”
Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”