Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Zekariya 6:1-15

6  Ndinakwezanso maso ndipo ndinaona magaleta anayi akubwera kuchokera pakati pa mapiri awiri. Mapiriwo anali amkuwa.  Galeta loyamba linali kukokedwa ndi mahatchi ofiira,+ ndipo galeta lachiwiri linali kukokedwa ndi mahatchi akuda.+  Galeta lachitatu linali kukokedwa ndi mahatchi oyera,+ ndipo galeta lachinayi linali kukokedwa ndi mahatchi amawangamawanga.+  Ndiyeno ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Kodi magaleta amenewa akuimira chiyani mbuyanga?”+  Mngeloyo anandiyankha kuti: “Magaletawa akuimira zolengedwa zauzimu zinayi+ zakumwamba zimene zikubwera+ pambuyo poimirira pamaso pa Ambuye+ wa dziko lonse lapansi.+  Mahatchi akuda amene akukoka galeta akupita kudziko la kumpoto.+ Mahatchi oyera akupita kutsidya la nyanja. Mahatchi amawangamawanga akupita kudziko la kum’mwera.+  Mahatchi amawangamawanga+ apitanso kukafufuza koti alowere kuti azikayendayenda mbali ina ya dziko lapansi.”+ Kenako iye anauza mahatchiwo kuti: “Pitani, mukayendeyende padziko lapansi.” Mahatchiwo anapita n’kumakayendayenda padziko lapansi.  Mngelo uja anandiitana mofuula n’kundiuza kuti: “Taona, mkwiyo+ umene Yehova anali nawo padziko la kumpoto watha chifukwa cha mahatchi amene apita kumeneko.”+  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 10  “Ukalandire chopereka kuchokera kwa anthu amene anatengedwa kupita kudziko lina.+ Ukalandire choperekacho kwa Heledai, Tobiya ndi Yedaya. Iweyo upite pa tsiku loikidwiratu, ndipo ukalowe m’nyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya,+ kumene kuli anthu ochokera ku Babulowo. 11  Pa choperekacho ukatengepo siliva ndi golide n’kupangira chisoti chachifumu chaulemerero.+ Chisoticho udzaveke Yoswa+ mkulu wa ansembe, mwana wa Yehozadaki. 12  Ndiyeno udzamuuze kuti, “‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Munthu uyu+ dzina lake ndi Mphukira.+ Adzaphuka pamalo ake ndipo adzamanga kachisi wa Yehova.+ 13  Munthu ameneyu adzamanga kachisi wa Yehova ndipo adzalandira ulemerero.+ Iye azidzalamulira atakhala pampando wake wachifumu ndipo adzakhalanso wansembe ali pampando womwewo.+ Maudindo awiri onsewo adzakhala ogwirizana.+ 14  Chisoti chachifumu chaulemererocho chizidzakhala m’kachisi wa Yehova kuti anthu azidzakumbukira+ Helemu, Tobiya, Yedaya+ ndi Heni mwana wa Zefaniya. 15  Anthu amene ali kutali, ndithu adzabwera kudzamanga nawo kachisi wa Yehova.”+ Anthu inu mukadzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu,+ mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa inu.’”+

Mawu a M'munsi