Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Zekariya 4:1-14

4  Mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja anabwerera n’kundidzutsa, ndipo ndinadzuka ngati munthu amene anali kugona.+  Kenako anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani?”+ Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona choikapo nyale chagolide yekhayekha.+ Pamwamba pake pali mbale yolowa. Choikapo nyalecho chili ndi nyale 7, inde, nyale 7.+ Nyale zimene zili pachoikapo nyalecho, zili ndi mapaipi 7.  M’mbali mwa choikapo nyalecho muli mitengo iwiri ya maolivi.+ Umodzi uli mbali ya kudzanja lamanja la mbale yolowayo, ndipo wina uli kumanzere kwa mbaleyo.”  Kenako ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Kodi zimenezi zikuimira chiyani mbuyanga?”+  Mngeloyo anandiyankha kuti: “Kodi sukudziwadi tanthauzo la zinthu zimenezi?” Pamenepo ine ndinati: “Inde sindikudziwa mbuyanga.”+  Choncho iye anandiuza kuti: “Yehova wauza Zerubabele kuti, ‘“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo,+ kapena mphamvu,+ koma mzimu wanga,”+ watero Yehova wa makamu.  Ngakhale pataikidwa chopinga chachikulu ngati phiri+ pamaso pa Zerubabele,+ chidzasalazidwa kukhala malo athyathyathya. Ndithu iye adzabweretsa mwala wotsiriza wa pakona.+ Akadzatero anthu adzafuula+ kuti: “Koma mwalawu ndiye ndi wokongola bwanji! Koma ndiye ndi wokongola!”’”+  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Manja a Zerubabele anayala maziko a nyumbayi,+ ndipo manja ake omwewo adzaimalizitsa.+ Pamenepo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa inu.+ 10  Munthu asakunyozeni chifukwa chakuti munayamba kumanga ndi zinthu zochepa.+ Anthu adzasangalala ndi ntchito imeneyi+ ndipo adzaona chingwe cha mmisiri womanga nyumba m’dzanja la Zerubabele. Maso 7 adzaona zimenezi. Maso 7 amenewa ndiwo maso a Yehova,+ ndipo akuyang’ana uku ndi uku padziko lonse lapansi.”+ 11  Ndiyeno ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Kodi mitengo iwiri ya maolivi, imene wina uli kudzanja lamanja ndi wina kumanzere kwa choikapo nyalechi, ikuimira chiyani?”+ 12  Ndinamufunsanso kuti: “Kodi nthambi ziwiri izi za mitengo ya maolivi, zimene zikuthira mafuta agolide m’mbale yolowa kudzera m’mapaipi awiri agolide, zikuimira chiyani?” 13  Iye anandiyankha kuti: “Kodi sukudziwadi tanthauzo la zinthu zimenezi?” Pamenepo ine ndinati: “Inde sindikudziwa mbuyanga.”+ 14  Ndipo iye anandiuza kuti: “Zinthu zimenezi zikuimira odzozedwa awiri+ amene amaimirira kumbali iyi ndi mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi.”+

Mawu a M'munsi