Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zekariya 12:1-14

12  Uthenga wokhudza Isiraeli: “Awa ndi mawu a Yehova okhudza Isiraeli.” Yehova, amene anatambasula miyamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi+ komanso kupanga mzimu+ n’kuuika mwa munthu, wanena kuti:  “Yerusalemu+ ndidzamusandutsa mbale yolowa yochititsa mitundu yonse ya anthu omuzungulira kuyenda dzandidzandi.+ Mdani adzazungulira Yuda, adzazungulira Yerusalemu.+  Pa tsiku limenelo,+ Yerusalemu ndidzamusandutsa mwala wotopetsa+ kwa anthu a mitundu yonse. Onse onyamula mwala umenewo, ndithu adzatemekatemeka koopsa. Anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adzasonkhana pamodzi kuti amuukire.+  Pa tsiku limenelo,+ ndidzachititsa hatchi+ iliyonse kudabwa kwambiri, ndipo wokwera pahatchiyo ndidzamuchititsa misala.+ Ndidzatsegula maso anga ndi kuyang’ana nyumba ya Yuda,+ ndipo hatchi iliyonse ya anthu a mitundu ina ndidzaichititsa khungu,” watero Yehova.  “Mafumu+ a Yuda adzanena mumtima mwawo kuti, ‘Anthu okhala mu Yerusalemu akutipatsa mphamvu zochokera kwa Mulungu wawo,+ Yehova wa makamu.’  Pa tsiku limenelo, ndidzachititsa mafumu a Yuda kukhala ngati mbaula zamoto pakati pa mitengo,+ komanso ngati miyuni yamoto pamilu ya tirigu wongodula kumene.+ Iwo adzatentha mitundu yonse ya anthu owazungulira, mbali ya kudzanja lamanja ndi kudzanja lamanzere.+ Anthu a mu Yerusalemu adzakhalabe mumzinda wawo wa Yerusalemu.+  “Choyamba, Yehova adzapulumutsa mahema a Yuda. Choncho kukongola kwa nyumba ya Davide ndi kukongola kwa anthu okhala mu Yerusalemu, sikudzakhala kwakukulu kwambiri kuposa kwa Yuda.  Pa tsiku limenelo, Yehova adzatchinjiriza anthu okhala mu Yerusalemu.+ Munthu amene wapunthwa pa tsiku limenelo, adzakhala wamphamvu ngati Davide.+ Nyumba ya Davide idzawatsogolera ngati Mulungu,+ ndiponso ngati mngelo wa Yehova.+  Pa tsiku limenelo, ndidzatsimikiza kuwononga mitundu yonse ya anthu imene ikubwera kudzaukira Yerusalemu.+ 10  “Posonyeza kuti ndakomera mtima nyumba ya Davide ndi anthu okhala mu Yerusalemu, ndidzawapatsa mzimu wanga+ umene udzawalimbikitse kundipempha mochonderera.+ Ndithu iwo adzayang’ana kwa munthu amene anamulasa,+ ndipo adzamulirira ngati mmene amachitira polirira mwana yekhayo wamwamuna. Adzamulira mowawidwa mtima ngati mmene amachitira polira maliro a mwana wamwamuna woyamba kubadwa.+ 11  Pa tsiku limenelo, anthu adzalira kwambiri mu Yerusalemu ngati mmene analirira ku Hadadirimoni, m’chigwa cha Megido.+ 12  Anthu a m’dziko lonselo adzalira mokuwa.+ Banja lililonse lizidzalira palokha. Banja la nyumba ya Davide lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’banja limeneli azidzalira paokha.+ Banja la nyumba ya Natani+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’banja limeneli azidzalira paokha. 13  Banja la nyumba ya Levi+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’banja limeneli azidzalira paokha. Banja la Asimeyi+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’banja limeneli azidzalira paokha. 14  Mabanja onse otsala adzalira. Banja lililonse lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’mabanjawo azidzalira paokha.+

Mawu a M'munsi