Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Zekariya 11:1-17

11  “Iwe Lebanoni,+ tsegula zitseko zako kuti moto utenthe mitengo yako ya mkungudza.+  Lira mofuula, iwe mtengo wofanana ndi mkungudza, chifukwa chakuti mtengo wa mkungudza wagwa, ndiponso mitengo ikuluikulu yawonongedwa.+ Lirani mofuula, inu mitengo ikuluikulu ya ku Basana, chifukwa nkhalango yowirira kwambiri ija yawonongedwa.+  Tamverani! Abusa akulira mofuula+ chifukwa ulemerero wawo watha.+ Tamverani! Mikango yamphamvu ikubangula mofuula chifukwa nkhalango zowirira, za m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano zawonongedwa.+  “Yehova Mulungu wanga wanena kuti, ‘Weta nkhosa zanga zimene zinayenera kuphedwa.+  Amene anazigula anazipha+ koma sanaimbidwe mlandu.+ Amene akuzigulitsa+ akunena kuti: “Yehova atamandike pamene ine ndikupeza chuma.”+ Abusa ake sazichitira chifundo ngakhale pang’ono.’+  “‘Sindidzachitiranso chifundo anthu okhala m’dzikoli,’+ watero Yehova. ‘Choncho ine ndichititsa aliyense kuti aponderezedwe ndi mnzake+ ndiponso mfumu yake.+ Iwo adzawononga dzikoli, ndipo ine sindidzapulumutsa aliyense m’manja mwawo.’”+  Choncho ine ndinayamba kuweta nkhosa+ zimene zinayenera kuphedwa,+ ndipo ndinachita zimenezi chifukwa cha inu, anthu osautsika a m’gulu la nkhosali.+ Chotero ndinatenga ndodo ziwiri.+ Imodzi ndinaipatsa dzina lakuti Wosangalatsa.+ Inayo ndinaipatsa dzina lakuti Mgwirizano,+ ndipo ndinayamba kuweta gulu la nkhosalo.  Kenako ndinachotsa abusa atatu m’mwezi umodzi+ chifukwa sindinathenso kuleza nawo mtima,+ ndipo iwonso ananyansidwa nane.  Pambuyo pake ndinanena kuti: “Ndileka kukuwetani.+ Amene akufa, afe.+ Amene akuwonongeka, awonongeke. Otsalawo adyane.”+ 10  Choncho ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Wosangalatsa+ ija ndi kuithyolathyola.+ Ndinachita izi kuti ndithetse pangano limene ndinapangana ndi anthu a mtundu wanga.+ 11  Panganolo linasweka pa tsiku limenelo. Mwa njira imeneyi, nkhosa zosautsika+ zimene zinali kundiona+ zinadziwa kuti zimene ndachitazo n’zimene Yehova ananena. 12  Kenako ndinawauza kuti: “Ngati mukuona kuti n’zoyenera,+ ndipatseni malipiro anga, koma ngati mukuona kuti n’zosayenera musandipatse.” Pamenepo iwo anandipatsa ndalama 30 zasiliva monga malipiro anga.+ 13  Zitatero Yehova anandiuza kuti: “Kaziponye mosungiramo chuma.+ Zimenezi ndi ndalama za mtengo wapatali zimene akuona kuti angandigule nazo.”+ Choncho ndinatenga ndalama 30 zasilivazo n’kukaziponya mosungiramo chuma panyumba ya Yehova.+ 14  Kenako ndinathyolathyola ndodo yanga yachiwiri ija yotchedwa Mgwirizano+ kuti ndithetse ubale+ wa Yuda ndi Isiraeli.+ 15  Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Tenga zida za m’busa wopanda pake.+ 16  Pakuti ndilola kuti m’dzikoli mukhale m’busa wina.+ M’busa ameneyu sadzasamala nkhosa zimene zikuwonongeka.+ Nkhosa yaing’ono sadzaifunafuna, ndipo yothyoka sadzaichiritsa.+ Nkhosa yotha kuima yokha sadzaipatsa chakudya, ndipo adzadya nyama ya nkhosa yonenepa.+ Iye adzakupula ziboda za nkhosazo.+ 17  Tsoka m’busa wanga wopanda pake+ amene akusiya nkhosa.+ Lupanga lidzamutema padzanja ndi kuboola diso lake la kudzanja lamanja. Dzanja lake lidzafota,+ ndipo diso lake la kudzanja lamanja lidzachita mdima.”

Mawu a M'munsi