Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Zekariya 1:1-21

1  M’mwezi wa 8, m’chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova analankhula ndi mneneri Zekariya,+ mwana wa Berekiya, mwana wa Ido,+ kuti:  “Yehova anakwiyira kwambiri makolo anu.+  “Uwauze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “‘Bwererani kwa ine,’+ watero Yehova wa makamu, ‘ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,’+ akutero Yehova wa makamu.”’  “‘Musakhale ngati makolo anu+ amene aneneri akale anawauza mofuula+ kuti: “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Chonde, siyani njira zanu zoipa ndi zochita zanu zoipa n’kubwerera kwa ine!’”’+ “‘Koma iwo sanamvere ndipo sanalabadire mawu anga,’+ watero Yehova.  “‘Kodi makolo anuwo ali kuti?+ Ndipo “kodi aneneriwo+ anapitirizabe kukhala ndi moyo mpaka kalekale?”*  Kodi zimene ndinalamula atumiki anga aneneri+ m’mawu anga ndi m’malangizo anga, sizinawachitikire makolo anu?’+ Chotero iwo anabwerera kwa ine ndi kunena kuti: ‘Yehova wa makamu watichitira zimene anakonza kuti atichitire+ mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+  Pa tsiku la 24, m’mwezi wa 11 womwe ndi mwezi wa Sebati, m’chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova anaonetsa masomphenya mneneri Zekariya,+ mwana wa Berekiya, mwana wa Ido.+ Masomphenya amene ndinaonawo ndi awa:  “Unali usiku pamene ndinaona munthu+ atakwera pahatchi* yofiira.+ Iye anaima chilili pakati pa mitengo ya mchisu+ imene inali m’chigwa. Kumbuyo kwake kunali mahatchi ofiirira, ofiira kwambiri ndi oyera.”+  Choncho, ine ndinafunsa kuti: “Kodi amenewa ndani mbuyanga?”+ Pamenepo mngelo amene anali kulankhula nane anandiyankha+ kuti: “Ine ndikuuza za amenewa.” 10  Kenako munthu amene anaima chilili pakati pa mitengo ya mchisu uja anayankha kuti: “Amenewa atumizidwa ndi Yehova kuti ayendeyende padziko lapansi.”+ 11  Ndiyeno iwo anauza mngelo wa Yehova amene anaima chilili pakati pa mitengo ya mchisu uja kuti: “Ife tayendayenda padziko lapansi+ ndipo taona kuti dziko lonse lapansi langokhala bata popanda chosokoneza.”+ 12  Choncho mngelo wa Yehova anati: “Inu Yehova wa makamu, kodi Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda imene munaikana ndi kuisiya kwa zaka 70,+ simuichitira chifundo kufikira liti?”+ 13  Yehova anayankha mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja. Anamuyankha ndi mawu abwino ndiponso olimbikitsa.+ 14  Ndiyeno mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja anandiuza kuti: “Fuula kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ndakhala ndikuchitira nsanje kwambiri Yerusalemu ndi Ziyoni.+ 15  Ndakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene akukhala mwabata.+ Ndawakwiyira chifukwa chakuti ine ndinangokwiyira anthu anga pang’ono pokha,+ koma anthu amenewa anakulitsa tsoka la anthu angawo.”’+ 16  “Choncho Yehova wanena kuti, ‘“Ndithu ndidzabwerera ku Yerusalemu ndi kuchitira chifundo mzinda umenewu.+ Nyumba yanga idzamangidwa mmenemo,+ ndipo chingwe choyezera chidzatambasulidwa pa Yerusalemu,”+ watero Yehova wa makamu.’ 17  “Fuulanso kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Mizinda yanga idzasefukira ndi zinthu zabwino.+ Yehova adzamva chisoni chifukwa cha tsoka limene anagwetsera Ziyoni+ ndipo adzasankhanso Yerusalemu.”’”+ 18  Kenako ndinaona nyanga zinayi m’masomphenya.+ 19  Choncho ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula nane uja kuti: “Kodi nyangazi zikutanthauza chiyani?” Iye anandiyankha kuti: “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda,+ Isiraeli+ ndi Yerusalemu.”+ 20  Yehova anandionetsanso amisiri anayi. 21  Pamenepo ndinafunsa kuti: “Kodi awa abwera kudzachita chiyani?” Mngeloyo anayankha kuti: “Zimenezi ndi nyanga+ zimene zinabalalitsa Yuda, moti panalibe amene anatha kudzutsa mutu wake. Amisiri awa adzabwera kudzaopseza nyangazi, kudzawononga nyanga za mitundu ina ya anthu imene ikukwezera nyanga* yawo dziko la Yuda kuti ibalalitse anthu ake.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”
Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.