Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Zefaniya 1:1-18

1  M’masiku a Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya Yuda, Yehova analankhula kudzera mwa Zefaniya mwana wa Kusa, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya. Iye anati:  “Ine ndidzafafaniza chilichonse chimene chili panthaka,” watero Yehova.  “Ndidzafafaniza anthu ndi nyama.+ Ndidzafafaniza zolengedwa zouluka m’mlengalenga, nsomba za m’nyanja,+ zokhumudwitsa pamodzi ndi anthu oipa,+ ndipo ndidzawononga anthu onse ndi kuwachotsa panthaka,”+ watero Yehova.  “Ndidzatambasula dzanja langa ndi kuwononga Yuda pamodzi ndi anthu onse okhala mu Yerusalemu. Ndidzawononga anthu onse otsala amene amapembedza Baala ndi kuwachotsa pamalo ano. Ndidzafafanizanso dzina la ansembe a mulungu wachilendo pamodzi ndi ansembe ena.  Ndidzafafaniza anthu amene akugwadira khamu la zinthu zakuthambo pamadenga* a nyumba zawo, ndiponso amene akugwada ndi kulumbira kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+ koma amakhalanso akulumbira m’dzina la Malikamu.  Ndidzafafaniza amene akusiya kutsatira Yehova, amene sanayesetse kuyandikira Yehova ndi amene sanafunsire kwa iye.”+  Khalani chete pamaso pa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa,+ pakuti tsiku la Yehova lili pafupi,+ ndipo Yehova wakonza nsembe+ moti wakonzekeretsa* anthu amene wawaitana.  “Ndiyeno pa tsiku limene Yehova adzapereka nsembe, ine ndidzalanga akalonga, ana a mfumu ndi onse ovala zovala zachilendo.  Pa tsiku limenelo, ndidzalanga aliyense amene ali pafupi ndi mpando wachifumu, anthu amene adzaza nyumba za ambuye awo ndi chiwawa ndiponso chinyengo. 10  Pa tsiku limenelo,” watero Yehova, “ku Chipata cha Nsomba kudzamveka phokoso la kulira ndipo kuchigawo chatsopano cha mzinda kudzamveka phokoso la kulira mokweza. Kumapiri kudzamveka phokoso la chiwonongeko chachikulu. 11  Lirani mofuula+ anthu inu okhala ku Makitesi, pakuti amalonda onse awonongedwa ndipo onse amene amayeza siliva pasikelo aphedwa. 12  “Pa nthawi imeneyo ndidzafufuza ndi nyale mu Yerusalemu mosamala kwambiri,+ ndipo ndidzalanga anthu amene akukhala mosatekeseka ngati vinyo amene nsenga zake zakhazikika pansi.+ M’mitima yawo, anthu amenewa akunena kuti, ‘Yehova sadzachita zabwino kapena kuchita zoipa.’+ 13  Chuma chawo chidzafunkhidwa ndipo nyumba zawo zidzakhala bwinja.+ Iwo adzamanga nyumba, koma sadzakhalamo.+ Iwo adzalima minda ya mpesa koma sadzamwa vinyo wochokera mmenemo.+ 14  “Tsiku lalikulu+ la Yehova lili pafupi.+ Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.+ Mkokomo wa tsiku la Yehova ukubwera ndi zowawa.+ Pa tsiku limenelo mwamuna wamphamvu adzalira.+ 15  Tsiku limenelo ndi tsiku lamkwiyo, tsiku lansautso ndi zowawa,+ tsiku la mphepo yamkuntho ndi losakaza, tsiku lamdima wochititsa mantha,+ tsiku lamitambo yakuda ndi lamdima wandiweyani. 16  Pa tsiku limenelo, lipenga la nyanga ya nkhosa ndiponso chizindikiro chochenjeza zidzalira+ pochenjeza mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, komanso nsanja zazitali kwambiri za m’makona.+ 17  Pamenepo ndidzasautsa mtundu wa anthu moti adzayenda ngati anthu akhungu+ chifukwa chakuti iwo achimwira Yehova.+ Magazi awo adzakhuthulidwa pansi ngati fumbi,+ ndipo matumbo awo adzakhuthulidwa pansi ngati ndowe.+ 18  Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+ Moto wa mkwiyo wake udzanyeketsa dziko lonse lapansi, chifukwa iye adzafafaniza anthu onse okhala padziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “patsindwi.”
Mawu ake enieni, “wayeretsa.”