Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yoweli 3:1-21

3  “Ndiyeno masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ ndidzabwezeretsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu amene anagwidwa ukapolo.+  Ine ndidzasonkhanitsanso pamodzi mitundu yonse ya anthu+ ndi kuibweretsa m’chigwa cha Yehosafati+ ndipo ndidzaiweruza chifukwa cha anthu anga ndi cholowa changa, Isiraeli.+ Mitundu imeneyi inamwaza Isiraeli pakati pa mitundu ya anthu ndiponso inagawana dziko langa.+  Mitunduyi inali kuchitira maere anthu anga+ ndipo inali kupereka mwana wamwamuna kuti akhale malipiro a hule.+ Inali kupereka mwana wamkazi kuti akhale malipiro a vinyo woti amwe.  “Tsopano ndili nawenso chiyani iwe Turo ndi Sidoni+ ndiponso inu nonse okhala m’chigawo cha Filisitiya?+ Kodi zimenezi ndi zimene mukundipatsa monga mphoto yanga? Ngati mukundipatsa zimenezi, ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+  Chifukwa chakuti anthu inu mwatenga siliva ndi golide wanga,+ mwabweretsa zinthu zanga zamtengo wapatali mu akachisi anu,+  mwagulitsa ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu+ kwa ana a Agiriki,+ ndi cholinga choti muwachotse ndi kuwapititsa kutali ndi dziko lawo,+  tsopano ndiwatenga kuti achoke kumalo amene munawagulitsa+ ndipo ndikubwezerani zimene munachita.+  Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa ana a Yuda.+ Ana a Yudawo adzawagulitsa kwa amuna a ku Sheba,+ mtundu wa anthu akutali.+ Ine Yehova ndanena zimenezi.  “Anthu inu, lengezani pakati pa mitundu ina kuti,+ ‘Konzekerani nkhondo! Konzekeretsani amuna amphamvu!+ Amuna onse ankhondo abwere!+ 10  Sulani makasu anu a pulawo kuti akhale malupanga, ndiponso zida zanu zosadzira mitengo+ kuti zikhale mikondo ing’onoing’ono. Munthu wofooka anene kuti: “Ndine mwamuna wamphamvu.”+ 11  Inu mitundu ya anthu yokhala mozungulira, bwerani mudzathandizane+ ndipo nonse musonkhane pamodzi.’”+ Inu Yehova, bweretsani ankhondo anu kumalo amenewo.+ 12  “Mitundu ya anthu inyamuke ndi kubwera kuchigwa cha Yehosafati,+ pakuti kumeneko ndidzakhala pansi kuti ndiweruze mitundu yonse ya anthu yokhala mozungulira.+ 13  “Yambani kumweta ndi chikwakwa,+ pakuti zokolola zacha.+ Bwerani, tsikirani kuno, pakuti moponderamo mphesa mwadzaza.+ Malo ogweramo vinyo wake asefukira, pakuti zoipa za anthu a mitundu ina zachuluka kwambiri.+ 14  Makamu ambirimbiri a anthu ali m’chigwa+ choweruzira mlandu, pakuti tsiku la Yehova layandikira m’chigwa choweruzira mlandu.+ 15  Dzuwa ndi mwezi zidzachita mdima, ndipo nyenyezi zidzasiya kuwala.+ 16  Yehova adzabangula ngati mkango kuchokera m’Ziyoni ndipo adzalankhula ali ku Yerusalemu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka+ koma Yehova adzakhala chitetezo kwa anthu ake,+ ndipo adzakhala malo a chitetezo champhamvu kwa ana a Isiraeli.+ 17  Pamenepo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu,+ amene ndimakhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika.+ Yerusalemu adzakhala malo anga opatulika,+ ndipo alendo sadzadutsanso mmenemo.+ 18  “Nthawi imeneyo mapiri adzachucha vinyo wotsekemera.+ Mkaka udzayenda pazitunda ndipo m’mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi. Kasupe wamadzi adzatuluka m’nyumba ya Yehova+ ndi kuthirira chigwa cha Mitengo ya Mthethe.+ 19  Iguputo adzasanduka bwinja,+ Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu+ chifukwa cha chiwawa chimene anachitira ana a Yuda, ndiponso chifukwa chokhetsa magazi osalakwa m’dziko la Yudalo.+ 20  Koma mu Yuda mudzakhala anthu mpaka kalekale,+ ndipo mu Yerusalemu mudzakhala anthu ku mibadwomibadwo.+ 21  Magazi awo amene anali ndi mlandu adzakhala opanda mlandu,+ ndipo Yehova azidzakhala mu Ziyoni.”+

Mawu a M'munsi