Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yoweli 1:1-20

1  Yehova analankhula+ kudzera mwa Yoweli mwana wa Petueli kuti:  “Tamverani inu akulu ndipo mutchere khutu inu nonse okhala m’dzikoli.+ Kodi zinthu izi zinachitikapo m’masiku anu, kapena m’masiku a makolo anu?+  Fotokozerani ana anu za zinthu zimenezi. Ana anu adzafotokozere ana awo, ndipo ana a ana anuwo adzafotokozerenso m’badwo wotsatira.  Zinthu zimene mbozi zinasiya zinadyedwa ndi dzombe. Zimene dzombelo linasiya zinadyedwa ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko ndipo zimene ana a dzombe oyenda pansiwo anasiya zinadyedwa ndi mphemvu.+  “Galamukani zidakwa inu.+ Lirani ndipo fuulani+ chifukwa cha vinyo wotsekemera*+ inu nonse okonda kumwa vinyo, pakuti vinyoyo wachotsedwa pakamwa panu.+  Pali mtundu umene walowa m’dziko langa. Mtunduwo ndi wamphamvu ndipo anthu ake ndi osawerengeka.+ Mano ndiponso nsagwadwa zawo zili ngati za mikango.+  Iwo achititsa mtengo wanga wa mpesa kukhala chinthu chodabwitsa+ ndipo mtengo wanga wa mkuyu ausandutsa chitsa.+ Nthambi za mitengo imeneyi azichotsa makungwa n’kuzitayira kutali.+ Mphukira zake azichotsa makungwa ndipo zauma.  Lirani momvetsa chisoni ngati mmene amalirira namwali amene wavala chiguduli*+ polirira mwamuna amene anali kufuna kumukwatira.  “Nsembe yambewu ndi nsembe yachakumwa zachotsedwa m’nyumba ya Yehova. Ansembe, atumiki a Yehova, alira.+ 10  Munda wawonongedwa+ ndipo nthaka ikulira pakuti mbewu zawonongedwa. Vinyo watsopano wauma+ ndipo mafuta atha.+ 11  Alimi achita manyazi+ chifukwa cha tirigu ndi barele ndipo osamalira minda ya mpesa akulira mofuula. Zili choncho chifukwa chakuti zokolola za m’munda zawonongeka.+ 12  Kukondwera kwachoka pamaso pa ana a anthu.+ Ndithu mtengo wa mpesa wauma ndiponso mtengo wa mkuyu wafota. Mtengo wa makangaza* komanso mtengo wa kanjedza, mtengo wa maapozi ndi mitengo yonse yakuthengo yauma. 13  “Dzimangirireni m’chiuno ndipo dzigugudeni pachifuwa,+ inu ansembe. Lirani mofuula, inu atumiki a paguwa lansembe. Lowani, valani ziguduli usiku wonse inu atumiki a Mulungu wanga, pakuti nsembe yambewu ndi nsembe yachakumwa zachotsedwa m’nyumba ya Mulungu wanu. 14  Konzekerani nthawi yosala kudya. Itanitsani msonkhano wapadera. Sonkhanitsani pamodzi akulu ndi anthu onse okhala m’dzikoli kuti akumane kunyumba ya Yehova Mulungu wanu ndipo alirire Yehova kuti awathandize. 15  “Kalanga ine! Tsiku lija likufika.+ Tsiku la Yehova lili pafupi.+ Tsikulo lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse. 16  Kodi chakudya sanatichotsere pamaso pathu? Kodi kukondwera ndi kusangalala sizinachotsedwe m’nyumba ya Mulungu wathu? 17  Nkhuyu zouma zawonongeka mafosholo ali pamwamba pake. Nkhokwe zawonongedwa. Nyumba zosungiramo zinthu zapasulidwa, pakuti mbewu zatha. 18  Ziweto zausa moyo. Gulu la ng’ombe likuyendayenda mosokonezeka pakuti kulibe msipu woti zidye. Ndiponso gulu la nkhosa ndi limene lalangidwa chifukwa cha uchimo. 19  “Ine ndidzaitana inu Yehova,+ pakuti moto wawononga malo odyetserako ziweto m’chipululu ndipo moto walawilawi wanyeketsa mitengo yonse yakuthengo.+ 20  Chifukwa chakuti mitsinje ya madzi yauma, ndipo moto wawononga malo odyetserako ziweto m’chipululu, zilombo zakutchire nazonso zikukufunani kwambiri.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “wonzuna.”
Ena amati “saka.”
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.