Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yoswa 7:1-26

7  Kenako, ana a Isiraeli anachimwa mwa kuphwanya lamulo lokhudza zinthu zoyenera kuwonongedwa. Anachimwa pamene Akani+ mwana wa Karami, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatengako zina mwa zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Chifukwa cha zimenezi, Yehova anakwiya kwambiri ndi ana a Isiraeli.+  Tsopano Yoswa anatumiza amuna ena kuchokera ku Yeriko kupita ku Ai,+ pafupi ndi Beti-aveni,+ kum’mawa kwa Beteli.+ Iye anawauza kuti: “Pitani kumeneko, mukazonde dzikolo.” Amunawo anapita, n’kukazonda dziko la Ai.+  Amunawo atabwerako anauza Yoswa kuti: “Musachite kutumiza anthu onse kumeneko. Mungotumiza amuna pafupifupi 2,000 kapena pafupifupi 3,000, kuti akakanthe Ai. Musatopetse anthu onse n’kupita kumeneko, pakuti kuli anthu ochepa.”  Choncho amuna pafupifupi 3,000 okha anapita kumeneko, koma anathawa popitikitsidwa ndi amuna a ku Ai.+  Ndipo amuna a ku Aiwo anapha amuna achiisiraeli pafupifupi 36. Anawathamangitsabe+ kuchokera kuchipata mpaka ku Sebarimu, n’kupitiriza kuwapha mpaka pamalo otsetsereka. Zitatero, mitima ya Aisiraeli onse inasungunuka ndi mantha.+  Yoswa ataona zimenezi anang’amba malaya ake. Kenako anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi+ patsogolo pa likasa la Yehova, mpaka madzulo. Anachita zimenezi pamodzi ndi akulu a Isiraeli, n’kumadzithira fumbi kumutu kwawo.+  Ndipo Yoswa anati: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, n’chifukwa chiyani mwayendetsa anthuwa mtunda wonsewu mpaka kudzawoloka mtsinje wa Yorodano, koma n’kutipereka m’manja mwa Aamori kuti atiphe? Ndiyetu mwina zikanakhala bwino tikanaganiza zongokhala kutsidya lina lija la Yorodano!+  Pepanitu Yehova, ndingatinso chiyani nanga, poona kuti Isiraeli wathawa pamaso pa adani ake?  Akanani ndi anthu onse a m’dziko lino adzamva zimenezi, ndipo adzatizinga ndithu, ndi kufafaniza dzina lathu kulichotsa padziko lapansi.+ Nanga zikatero mudzaliteteza bwanji dzina lanu lalikulu?”+ 10  Tsopano Yehova anauza Yoswa kuti: “Dzuka iwe! N’chifukwa chiyani wadzigwetsa mpaka nkhope yako pansi? 11  Aisiraeli achimwa, ndiponso aphwanya pangano+ limene ndinawalamula kuti alisunge. Iwo atenga zina mwa zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Aba+ zinthuzo ndi kuzibisa+ pakati pa katundu wawo.+ 12  Ana a Isiraeli sadzathanso kulimbana ndi adani awo.+ Iwo azingothawa kwa adani awo, chifukwa iwonso akhala zinthu zoyenera kuwonongedwa. Sindidzakhalanso nanu kufikira mutachotsa pakati panu zinthu zoyenera kuwonongedwazo.+ 13  Dzuka! Yeretsa anthuwa,+ uwauze kuti, ‘Mawa mudziyeretse, pakuti Yehova, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Kalanga Isiraeli, pakati panu pali zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Anthu inu simudzathanso kulimbana ndi adani anu, kufikira mutachotsa pakati panu zinthu zoyenera kuwonongedwazo. 14  Mawa m’mawa, mubwere fuko ndi fuko. Fuko limene Yehova adzasankhe+ lidzabwere patsogolo. Kenako mbumba ndi mbumba, ndipo mbumba imene Yehova adzasankhe idzabwere patsogolo. Kenako banja ndi banja, ndipo banja limene Yehova adzasankhe lidzabwere patsogolo, komanso mwamuna aliyense wamphamvu payekhapayekha. 15  Amene apezeke ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo, adzatenthedwa ndi moto,+ iye limodzi ndi banja lake ndi zonse ali nazo. Adzatenthedwa chifukwa waphwanya pangano la Yehova,+ ndiponso wachita cholakwa chochititsa manyazi mu Isiraeli.”’”+ 16  Ndiyeno Yoswa anadzuka m’mawa kwambiri, n’kuuza Isiraeli kuti afike pamaso pa Mulungu, fuko ndi fuko, ndipo fuko la Yuda linasankhidwa. 17  Kenako anauza mabanja a m’fuko la Yuda kufika pamaso pa Mulungu, ndipo banja la Zera linasankhidwa. Kenako anauza banja la Zera+ kufika pamaso pa Mulungu, mwamuna aliyense wamphamvu payekhapayekha, ndipo Zabidi anasankhidwa. 18  Potsirizira pake anauza a m’nyumba ya Zabidi kufika pamaso pa Mulungu, mwamuna aliyense wamphamvu payekhapayekha. Ndipo Akani mwana wa Karami, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anasankhidwa.+ 19  Tsopano Yoswa anauza Akani kuti: “Mwana wanga, chonde, lemekeza Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ ulula kwa iye.+ Tandiuza+ chonde, n’chiyani chimene wachita? Usandibisire.”+ 20  Ndipo Akani anayankha Yoswa kuti: “Ndithu ndam’chimwira Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ Zimene ndinachita ndi izi: 21  Nditaona+ chovala chamtengo wapatali cha ku Sinara,+ pakati pa katundu wotsalayo, chokongola m’maonekedwe, komanso masekeli* a siliva 200, ndi mtanda umodzi wa golide wolemera masekeli 50, ndinazikhumba zinthuzo,+ ndipo ndinazitenga.+ Panopo chovalacho ndinachikumbira pansi, pakati pa hema wanga, pamodzi ndi ndalamazo, ndipo ndalamazo zili pansi pa chovalacho.”+ 22  Nthawi yomweyo Yoswa anatuma anthu, amene anathamangira kuhemako. Iwo anachipezadi chovalacho m’hema wake, ndi ndalama zija pansi pake. 23  Anthu aja anatenga zinthuzo pakati pa hemayo, n’kubwera nazo kwa Yoswa ndi ana a Isiraeli onse, kumene anazikhuthulira pansi pamaso pa Yehova. 24  Tsopano Yoswa ndi Aisiraeli onse anatenga Akani+ mwana wa Zera, limodzi ndi siliva uja, chovala chamtengo wapatali chija, mtanda wa golide uja,+ komanso ana ake aamuna ndi aakazi, ng’ombe zake, abulu, nkhosa, ndiponso hema wake, ndi chilichonse chomwe chinali chake, n’kutsikira nawo kuchigwa cha Akori.+ 25  Ndiyeno Yoswa anati: “N’chifukwa chiyani wachititsa kuti tinyanyalidwe?+ Iweyo lero Yehova akunyanyala.” Atatero, Aisiraeli onse anawaponya miyala,+ kenako anawatentha ndi moto.+ Choncho, anawaponya miyala. 26  Pambuyo pake, anaunjika mulu waukulu wa miyala pa iye. Muluwo ulipo mpaka lero.+ Zitatero, mkwiyo waukulu wa Yehova unatha.+ Ndiye chifukwa chake malowo anatchedwa chigwa cha Akori*+ mpaka lero.

Mawu a M'munsi

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Dzina lakuti “Akori” limatanthauza “Kunyanyalidwa” kapena “Mavuto.”