Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yoswa 6:1-27

6  Mzinda wa Yeriko unatsekedwa mwamphamvu chifukwa cha ana a Isiraeli. Palibe amene anali kutuluka kapena kulowa mumzindawo.+  Ndipo Yehova anauza Yoswa kuti: “Taona! Mzinda wa Yeriko ndaupereka m’manja mwako, pamodzi ndi mfumu yake ndi asilikali ake amphamvu ndi olimba mtima.+  Tsopano, amuna ankhondo nonsenu, mugube kuzungulira mzindawu kamodzi. Muchite zimenezi kwa masiku 6.  Ansembe 7 aziyenda patsogolo pa Likasa atanyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa zamphongo. Pa tsiku la 7 mudzagube kuzungulira mzindawo maulendo 7, ansembewo akuliza malipenga.+  Ansembewo akadzaliza malipenga a nyanga za nkhosa, ndipo inu mukadzamva kulira kwa malipengawo, nonse mudzafuule mfuu yankhondo mwamphamvu,+ ndipo mpanda wonse wa mzindawo udzagwa pansi.+ Pamenepo, nonsenu mudzathamangire kumeneko.”  Chotero Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe+ n’kuwauza kuti: “Nyamulani likasa la pangano,+ ndipo ansembe 7 aziyenda patsogolo pa likasa+ la Yehovalo. Ansembewo atenge malipenga 7 a nyanga za nkhosa zamphongo.”  Anauzanso asilikaliwo kuti: “Nyamukani, mukagube kuzungulira mzindawo. Gulu la asilikali onyamula zida zankhondo+ likhale patsogolo pa likasa la Yehova.”  Monga Yoswa ananenera, ansembe 7 ananyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa pamaso pa Yehova. Iwo anatsogola akuliza malipenga awo, ndipo likasa la pangano la Yehova linali kuwatsatira pambuyo pawo.  Gulu la asilikali onyamula zida linali kuyenda patsogolo pa ansembe oimba malipenga, pamene gulu lina la asilikali linali kubwera pambuyo+ pa Likasa, kwinaku malipenga akuimbidwa mosalekeza. 10  Yoswa analamula asilikaliwo+ kuti: “Musafuule kapena kulankhula kanthu, ndipo pakamwa panu pasatuluke mawu alionse kufikira tsiku limene ndidzakuuzani kuti, ‘Fuulani!’ Pamenepo mudzafuule.”+ 11  Chotero iye atalamula, likasa la Yehova linazungulira mzindawo kamodzi, asilikaliwo akuguba nalo. Pambuyo pake, iwo anapita kumsasa ndipo anakhala kumeneko usiku wonse. 12  Tsiku lotsatira, Yoswa anadzuka m’mawa kwambiri,+ ndipo ansembe ananyamula likasa+ la Yehova. 13  Ansembe 7 onyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa, omwe anali kukhala patsogolo pa likasa la Yehova, anali kuyenda akuliza malipenga mosalekeza. Patsogolo pawo panali gulu la asilikali onyamula zida, ndipo pambuyo pa likasa la Yehova panali kubwera asilikali ena, malipenga akulira mosalekeza.+ 14  Iwo anagubanso kuzungulira mzindawo kamodzi pa tsiku lachiwirili. Atamaliza kuzungulira anabwerera kumsasa. Anachita zimenezi kwa masiku 6.+ 15  Pa tsiku 7, anadzuka m’mawa kutangoyamba kucha, ndipo anaguba kuzungulira mzindawo monga anali kuchitira. Pa tsiku la 7 limeneli, anazungulira mzindawo maulendo 7.+ 16  Pa ulendo wa 7 wozungulira mzindawo, ansembe aja analiza malipenga awo, ndipo Yoswa anauza asilikaliwo kuti: “Fuulani!+ Pakuti Yehova wakupatsani mzindawu.+ 17  Mzindawu wapatulidwa kuti uwonongedwe,+ pakuti mzindawu limodzi ndi zonse zili mmenemo ndi za Yehova. Rahabi+ yekha, hule uja, musamuphe. Mum’siye ndi moyo, iye pamodzi ndi onse amene ali naye m’nyumba mwake, chifukwa iye anabisa azondi amene tinawatuma.+ 18  Koma zinthu zoyenera kuwonongedwa musamale nazo,+ kuopera kuti mungazikhumbire+ n’kutengako zinthuzo,+ n’kuchititsa msasa wa Isiraeli nawonso kukhala chinthu choyenera kuwonongedwa ndi kunyanyalidwa.+ 19  Siliva, golide, ndi zipangizo zamkuwa ndi zachitsulo, zonse n’zopatulika kwa Yehova.+ Ziyenera kupita ku chuma cha Yehova.”+ 20  Ansembe aja ataliza malipenga awo,+ asilikaliwo anafuula. Atangomva kulira kwa malipenga, anayamba kufuula mwamphamvu mfuu yankhondo, ndipo mpanda wa mzindawo unayamba kugwa mpaka pansi.+ Zitatero, iwo analowa mumzindawo. Aliyense anathamangira kumeneko, ndi kulanda mzindawo. 21  Aliyense amene anali mumzindawo anamupha ndi lupanga, kuyambira amuna, akazi, anyamata ndi nkhalamba zomwe. Anaphanso ng’ombe, nkhosa, ndi abulu.+ 22  Ndiyeno Yoswa anauza amuna awiri aja amene anakazonda dzikolo, kuti: “Pitani kunyumba kwa mayi uja, hule uja, mukam’tulutse limodzi ndi onse amene ali naye, monga momwe munalumbirira kwa iye.”+ 23  Chotero, anyamata amene anakazonda dziko aja, anapita kukatulutsa Rahabi, bambo ake, mayi ake, alongo ake, ndi onse amene anali naye. Anatulutsa achibale ake onse,+ ndipo anawapatsa malo kunja kwa msasa wa Isiraeli. 24  Atatero, anatentha ndi moto mzindawo ndi zonse zimene zinali mmenemo.+ Koma siliva, golide, zipangizo zamkuwa ndi zachitsulo, anazipereka kuti zipite ku chuma cha nyumba ya Yehova.+ 25  Ndipo Rahabi hule uja, limodzi ndi anthu a m’nyumba ya bambo ake, ndi onse amene anali naye, Yoswa sanawaphe.+ Kufikira lero, mayiyo akukhalabe pakati pa Aisiraeli,+ chifukwa anabisa anyamata amene Yoswa anawatuma kukazonda Yeriko.+ 26  Ndiyeno pa nthawiyo, Yoswa analumbira kuti: “Adzakhale wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzamangenso mzinda wa Yerikowu. Akadzangoyala maziko ake, mwana wake woyamba adzafe, ndipo akadzaika zitseko zake za pachipata, mwana wake wotsiriza adzafe.”+ 27  Chotero Yehova anakhaladi ndi Yoswa,+ ndipo mbiri yake inamveka padziko lonse lapansi.+

Mawu a M'munsi