Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yoswa 5:1-15

5  Mafumu onse a Aamori+ amene anali kutsidya la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, ndi mafumu onse a Akanani+ amene anali m’mphepete mwa nyanja, anamva zakuti Yehova anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano pamaso pa ana a Isiraeli kufikira atawoloka. Atamva zimenezo, mitima yawo inasungunuka ndi mantha,+ moti anatheratu mphamvu poopa ana a Isiraeli.+  Pa nthawi imeneyo, Yehova anauza Yoswa kuti: “Panga timipeni tamiyala kuti udule khungu+ la ana a Isiraeli kachiwiri.”  Chotero Yoswa anapanga timipeni tamiyala, ndipo anadula khungu la ana a Isiraeli. Zimenezi zinachitikira ku Gibeyati-haaraloti.+  Yoswa anadula khungu la ana a Isiraeliwo chifukwa chakuti anthu onse amene anatuluka mu Iguputo, amuna onse otha kupita kunkhondo, anali atafera+ m’chipululu pa ulendo wochokera ku Iguputo.  Anthu onse amene anatuluka mu Iguputo anali odulidwa. Koma onse amene anabadwira m’chipululu pa ulendo wochokera ku Iguputo, sanadulidwe.  Ana a Isiraeliwo anayenda m’chipululu zaka 40,+ mpaka amuna onse otha kupita kunkhondo amene anatuluka mu Iguputo atatha, amene sanamvere mawu a Yehova. Amenewo Yehova anawalumbirira kuti sadzawalola kuona dziko+ limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzalipereka kwa anthu ake,*+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+  Iye analowetsa m’dzikomo ana awo m’malo mwa makolowo.+ Ana amenewa Yoswa anawadula khungu, chifukwa sanadulidwe pa nthawi imene anali pa ulendo.  Atamaliza kuchita mdulidwe pamtundu wonsewo, anthuwo anakhala m’malo awo mumsasa mpaka atachira.+  Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: “Lero ndachotsa chitonzo cha Iguputo pa inu.”+ Chotero malowo anayamba kuwatchula kuti Giligala,+ kufikira lero. 10  Ana a Isiraeliwo anakhalabe ku Giligala. Anachita pasika madzulo pa tsiku la 14 la mweziwo,+ ali m’chipululu cha Yeriko. 11  Tsiku lotsatira, iwo anayamba kudya zokolola za m’dzikomo. Pa tsikuli anayamba kudya mikate yopanda chofufumitsa+ ndiponso tirigu wokazinga. 12  Mana analeka kugwa pa tsikuli, pamene ana a Isiraeli anadya zokolola za m’dzikomo. Kuyambira pamenepo, mana sanagwenso pakati pa ana a Isiraeli.+ Chotero, chaka chimenechi n’chimene iwo anayamba kudya zokolola za m’dziko la Kanani.+ 13  Tsiku lina Yoswa ali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo anaona mwamuna wina+ ataima potero patsogolo pake, ali ndi lupanga m’dzanja lake.+ Pamenepo Yoswa anayandikira munthuyo ndi kumufunsa kuti: “Kodi uli kumbali yathu kapena kumbali ya adani athu?” 14  Munthuyo anayankha kuti: “Iyayi, koma ine pokhala kalonga wa gulu lankhondo la Yehova, tsopano ndabwera.”+ Yoswa atamva mawu amenewo, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ ndipo anamuuza kuti: “Lankhulani mbuyanga kwa kapolo wanu.” 15  Ndiyeno kalonga wa gulu lankhondo la Yehovayo anauza Yoswa kuti: “Vula nsapato zako, chifukwa malo amene waimapowo ndi oyera.” Nthawi yomweyo, Yoswa anavula nsapato zake.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “kwa ife.”