Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yoswa 19:1-51

19  Maere+ achiwiri anagwera Simiyoni, kapena kuti fuko la ana a Simiyoni,+ potsata mabanja awo. Cholowa chawo chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda.+  M’gawo la cholowa chawo munali Beere-seba+ kuphatikizapo Sheba, Molada,+  Hazara-suali,+ Bala, Ezemu,+  Elitoladi,+ Betuli, Horima,  Zikilaga,+ Beti-marikaboti, Hazara-susa,+  Beti-lebaoti,+ ndi Saruheni. Mizinda 13 ndi midzi yake.  Munalinso Aini,+ Rimoni,+ Eteri, ndi Asani.+ Mizinda inayi ndi midzi yake,  ndiponso midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka kukafika ku Baalati-beere,+ komwe ndi ku Rama+ wa kum’mwera. Ichi chinali cholowa cha fuko la ana a Simiyoni potsata mabanja awo.  Cholowa cha ana a Simiyoni chinali m’gawo la ana a Yuda chifukwa ana a Yuda gawo lawo linawakulira.+ Choncho ana a Simiyoni anapatsidwa malo pakati pa cholowa chawo.+ 10  Maere achitatu+ anagwera ana a Zebuloni+ potsata mabanja awo. Malire a cholowa chawo anayambira ku Saridi 11  n’kulowera chakumadzulo, kukafika ku Marala. Anapitirira kukafika ku Dabeseti mpaka kuchigwa chimene chili kutsogolo kwa Yokineamu.+ 12  Kenako malirewo anakhota n’kubwerera kulowera kum’mawa kwa Saridi mpaka kumalire a Kisilotu-tabori. Ndiyeno anapitirira kukafika ku Daberati+ mpaka ku Yafiya. 13  Kuchokera kumeneko, malirewo analowera chakum’mawa n’kukafika ku Gati-heferi,+ ku Eti-kazini, ndi ku Rimoni, mpaka ku Nea. 14  Malirewo anazungulira kumpoto kwa Nea kukafika ku Hanatoni, n’kukathera kuchigwa cha Ifita-eli, 15  komanso ku Katati, Nahalala, Simironi,+ Idala, ndi ku Betelehemu.+ Mizindayi inalipo 12 ndi midzi yake. 16  Ichi chinali cholowa+ cha ana a Zebuloni potsata mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake. 17  Maere achinayi anagwera Isakara,+ kapena kuti ana a Isakara potsata mabanja awo. 18  Malire a gawo lawo anakafika ku Yezereeli,+ Kesulotu, Sunemu,+ 19  Hafaraimu, Sioni, Anaharati, 20  Rabiti, Kisioni, Ebezi, 21  Remeti, Eni-ganimu,+ Eni-hada, ndi Beti-pazezi. 22  Malirewo anakafika ku Tabori,+ ku Sahazuma, ndi ku Beti-semesi n’kukathera ku Yorodano. Mizinda 16 ndi midzi yake. 23  Ichi chinali cholowa cha fuko la ana a Isakara potsata mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake. 24  Maere achisanu+ anagwera fuko la ana a Aseri,+ potsata mabanja awo. 25  Malire a gawo lawo anadutsa ku Helikati,+ Hali, Beteni, Akasafu,+ 26  Alameleki, Amadi, ndi Misali.+ Analowera chakumadzulo ku Karimeli+ ndi ku Sihori-libanati. 27  Kenako anakhota n’kubwerera kulowera kotulukira dzuwa ku Beti-dagoni, n’kukafika ku Zebuloni+ ndi kumpoto kwa chigwa cha Ifita-eli. Anakafikanso ku Beti-emeki ndi ku Nehieli n’kupitirira mpaka ku Kabulu chakumanzere. 28  Anapitirira mpaka ku Eburoni, Rehobu, Hamoni, Kana, mpaka kumzinda wa anthu ambiri wa Sidoni.+ 29  Malirewo anakhota n’kubwerera ku Rama, mpaka kukafika kumzinda wa Turo+ wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Kenako anakhotanso n’kubwerera ku Hosa n’kukathera kunyanja, m’chigawo cha Akizibu.+ 30  Anakafikanso ku Uma, Afeki,+ ndi Rehobu.+ Mizindayi inalipo 22 ndi midzi yake. 31  Ichi chinali cholowa cha fuko la ana a Aseri potsata mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake. 32  Maere a 6+ anagwera ana a Nafitali+ potsata mabanja awo. 33  Malire a gawo lawo anayambira ku Helefi, ndi kumtengo waukulu wa ku Zaananimu,+ mpaka ku Adami-nekebi, ndi ku Yabineeli, n’kukafika ku Lakumu n’kukathera ku Yorodano. 34  Malirewo anakhotera kumadzulo n’kubwerera ku Azinotu-tabori, n’kupitirira mpaka kukafika ku Hukoku ndi ku Zebuloni+ kum’mwera. Anakafikanso ku Aseri+ kumadzulo, ndi kotulukira dzuwa ku Yuda,+ kumtsinje wa Yorodano. 35  Mizinda yake yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri inali Zidimu, Zere, Hamati,+ Rakati, Kinereti,+ 36  Adama, Rama, Hazori,+ 37  Kedesi,+ Edirei, Eni-hazori, 38  Yironi, Migidala-eli, Horemu, Beti-anati, ndi Beti-semesi.+ Mizinda 19 ndi midzi yake. 39  Ichi chinali cholowa+ cha fuko la ana a Nafitali potsata mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake. 40  Maere a 7+ anagwera fuko la ana a Dani+ potsata mabanja awo. 41  Malire a gawo la cholowa chawo anadutsa ku Zora,+ Esitaoli, Iri-semesi, 42  Saalabini,+ Aijaloni,+ Itila, 43  Eloni, Timuna,+ Ekironi,+ 44  Eliteke, Gebetoni,+ Baalati,+ 45  Yehuda, Bene-beraki, Gati-rimoni,+ 46  Me-jarikoni, Rakoni, n’kukafika kumalire amene ali kutsogolo kwa Yopa.+ 47  Gawo la ana a Dani linawachepera,+ choncho anapita kukachita nkhondo ku Lesemu.+ Analanda mzindawo n’kupha anthu ake ndi lupanga. Kenako anautenga n’kuyamba kukhalamo ndipo anautcha Lesemu Dani, potengera dzina la kholo lawo Dani.+ 48  Ichi chinali cholowa cha fuko la ana a Dani potsata mabanja awo, ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake. 49  Apa m’pamene anamalizira kugawa dzikolo m’zigawozigawo kuti akhalemo. Kenako ana a Isiraeli anam’patsa cholowa Yoswa mwana wa Nuni pakati pawo. 50  Molamulidwa ndi Yehova, anam’patsa mzinda umene anapempha+ wa Timinati-sera,+ m’dera lamapiri la Efuraimu ndipo iye anayamba kumanga mzindawo n’kumakhalamo. 51  Zimenezi ndiye zigawo za cholowa chimene wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mafuko a ana a Isiraeli, anagawira anthu.+ Anagawa dzikolo pochita maere ku Silo+ pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako,+ ndipo anamaliza kuligawa dzikolo.

Mawu a M'munsi