Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yoswa 18:1-28

18  Kenako khamu lonse la ana a Isiraeli linasonkhana ku Silo,+ ndipo kumeneko anamangako chihema chokumanako,+ popeza anali atagonjetsa dziko lomwe linali pamaso pawo.+  Koma mafuko 7 a ana a Isiraeli anali asanagawiridwe cholowa.  Choncho Yoswa anafunsa ana a Isiraeli kuti: “Kodi muzengereza mpaka liti osapita kukalanda dziko+ limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani?+  Sankhani amuna atatu pafuko lililonse oti ndiwatume apite akayendere dzikolo. Akalembe mmene dzikolo lilili kuti lidzagawidwe monga cholowa cha mafuko awo, akakatero adzabwerere kwa ine.+  Ndiyeno adzagawane dzikolo poligawa m’zigawo 7.+ Fuko la Yuda lidzakhalabe kugawo lawo kum’mwera,+ ndipo a nyumba ya Yosefe adzakhalabe kugawo lawo kumpoto.+  Koma anthu inu, mukagawe dzikolo m’zigawo 7 ndipo mukazilembe. Mukakatero, mukabwere nazo kuno kwa ine kuti ndidzakuchitireni maere+ pamaso pa Yehova Mulungu wathu.  Alevi alibe gawo pakati panu,+ chifukwa cholowa chawo ndi unsembe wa Yehova.+ Fuko la Gadi, Rubeni,+ ndi hafu ya fuko la Manase+ analandira kale cholowa chawo, chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa kutsidya la kum’mawa la Yorodano.”+  Choncho amuna opita kukalemba dzikowo ananyamuka kuti azipita, ndipo Yoswa anawalamula+ kuti: “Pitani mukayendere dzikolo n’kulemba mmene lilili. Mukatero mubwerere kwa ine, ndipo ineyo ndidzakuchitirani maere+ pamaso pa Yehova kuno ku Silo.”+  Pamenepo amunawo anapitadi kukayendera dzikolo. Anakaligawa+ m’zigawo 7 potsatira mizinda yake, n’kulemba m’buku. Atamaliza, anapita kwa Yoswa kumsasa ku Silo, 10  ndipo Yoswa anawachitira maere pamaso pa Yehova+ ku Silo. Kumeneko Yoswa anagawa dzikolo n’kupereka gawo limodzilimodzi ku mafuko a ana a Isiraeli.+ 11  Maere+ oyamba anagwera fuko la ana a Benjamini+ potsata mabanja awo, ndipo gawo limene anapatsidwa linali pakati pa ana a Yuda+ ndi ana a Yosefe.+ 12  Malire a gawo lawo kumpoto anayambira ku Yorodano, n’kupitirira kukafika kumalo otsetsereka a kumpoto kwa Yeriko,+ n’kukwera phiri chakumadzulo, n’kukathera kuchipululu cha Beti-aveni.+ 13  Malirewo anapitirira kukafika ku Luzi,+ kutanthauza Beteli.+ Anakafika kum’mwera kwa malo otsetsereka otchedwa Luzi, n’kutsetserekera ku Ataroti-adara,+ n’kukadutsa paphiri la kum’mwera kwa Beti-horoni Wakumunsi.+ 14  Kumadzulo kwa gawolo, malirewo anakhotera kum’mwera, paphiri loyang’anizana ndi kum’mwera kwa Beti-horoni. Kuchokera pamenepo anakathera ku Kiriyati-baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu,+ womwe ndi mzinda wa ana a Yuda. Awa ndiwo malire a kumadzulo a gawo la Benjamini. 15  Malire a kum’mwera a gawolo anayambira kumapeto kwa Kiriyati-yearimu, n’kulowera chakumadzulo, n’kupitirira kukafika kukasupe wa madzi a Nafitoa.+ 16  Malirewo anatsetserekera kuphiri loyang’anizana ndi chigwa cha mwana wa Hinomu,+ limene linathera kumpoto kwa chigwa cha Arefai.+ Kenako anatsetserekera kuchigwa cha Hinomu kum’mwera kwa malo otsetsereka otchedwa Yebusi,+ n’kutsetserekabe mpaka ku Eni-rogeli.+ 17  Analowera chakumpoto n’kukafika ku Eni-semesi mpaka ku Gelilotu, yemwe ali kutsogolo kwa chitunda cha Adumi.+ Kuchokera pamenepo, anatsetserekera kumwala+ wa Bohani,+ mwana wa Rubeni. 18  Ndiyeno anakafika kumalo otsetsereka a kumpoto amene ali kutsogolo kwa Araba, n’kutsetserekera ku Araba. 19  Malirewo anapitirira mpaka kumalo otsetsereka a kumpoto kwa Beti-hogila,+ n’kukathera kugombe la kumpoto kwa Nyanja Yamchere,+ kumapeto a kum’mwera a mtsinje wa Yorodano. Awa anali malire a kum’mwera a gawo la Benjamini. 20  Kum’mawa, malire ake anali mtsinje wa Yorodano. Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini potsata mabanja awo, ndi malire ake kuzungulira gawo lonse. 21  Mizinda ya fuko la ana a Benjamini potsata mabanja awo inali Yeriko,+ Beti-hogila, Emeki-kezizi, 22  Beti-araba,+ Zemaraimu, Beteli,+ 23  Aavi, Para, Ofira,+ 24  Kefara-amoni, Ofini, ndi Geba.+ Mizinda 12 ndi midzi yake. 25  Kunalinso Gibeoni,+ Rama, Beeroti, 26  Mizipe,+ Kefira,+ Moza, 27  Rekemu, Iripeeli, Tarala, 28  Zela,+ Ha-elefi, Yebusi, kutanthauza Yerusalemu,+ Gibea,+ ndi Kiriyati. Mizinda 14 ndi midzi yake. Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini potsata mabanja awo.+

Mawu a M'munsi