Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yoswa 16:1-10

16  Malire a gawo+ la ana a Yosefe+ anayambira kumtsinje wa Yorodano+ kufupi ndi Yeriko kukafika kumadzi a Yeriko chakum’mawa, mpaka kuchipululu chochokera ku Yeriko kukafika kudera lamapiri la Beteli.+  Atachoka ku Beteli wa ku Luzi,+ malirewo anakadutsa kumalire a Aareki+ ku Ataroti.  Kenako anatsetserekera kumadzulo kumalire a Ayafeleti, mpaka kukafika kumalire a Beti-horoni Wakumunsi+ ndi Gezeri,+ n’kukathera kunyanja.+  Ana a Yosefe,+ omwe ndi Manase ndi Efuraimu,+ analandira gawo lawo.+  Malire a kum’mawa a cholowa cha ana a Efuraimu potsata mabanja awo, anali Ataroti-adara+ mpaka kukafika ku Beti-horoni Wakumtunda,+  n’kukathera kunyanja. Kumpoto kwake kunali Mikametatu,+ ndipo malirewo anazungulira chakum’mawa kukafika ku Taanatu-silo, n’kupitirirabe chakum’mawa mpaka ku Yanoa.  Ndiyeno anatsetsereka kuchoka ku Yanoa kukafika ku Ataroti ndi ku Naara mpaka ku Yeriko,+ n’kupitirirabe mpaka ku Yorodano.  Kuchoka ku Tapuwa,+ malirewo analowera chakumadzulo kuchigwa cha Kana+ n’kukathera kunyanja.+ Chimenechi ndi cholowa cha fuko la ana a Efuraimu potsata mabanja awo.  Cholowacho chinaphatikizapo mizinda yonse ndi midzi ya ana a Efuraimu+ imene inali mkati mwa cholowa cha ana a Manase. 10  Aefuraimu analephera kupitikitsa Akanani+ amene anali kukhala ku Gezeri.+ Choncho Akananiwo akukhalabe pakati pa Aefuraimu mpaka lero,+ ndipo anayamba kuwagwiritsa ntchito yaukapolo.+

Mawu a M'munsi