Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yoswa 14:1-15

14  Limeneli ndilo dziko limene ana a Isiraeli anatenga monga cholowa chawo m’dziko la Kanani.+ Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mafuko a makolo a ana a Isiraeli, ndiwo anagawa dzikolo kuti likhale cholowa chawo.+  Anagawira cholowacho mafuko 9 ndi hafu, mwa kuchita maere,+ monga mmene Yehova analamulira kudzera mwa Mose.+  Mose anali atagawira kale cholowa mafuko awiri ndi hafu kutsidya lina la Yorodano.+ Koma Alevi sanawapatse cholowa pakati pawo.+  Ana a Yosefe anakhala mafuko awiri,+ la Manase+ ndi la Efuraimu.+ Iwowa anapatsa Alevi mizinda+ yoti azikhalamo, malo odyetserako ziweto, ndi osungirako katundu wawo, koma sanawagawire cholowa cha malo.+  Ana a Isiraeli anagawadi dzikolo monga mmene Yehova analamulira Mose.  Tsopano ana a Yuda anapita kwa Yoswa ku Giligala.+ Ndipo Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi,+ anauza Yoswa kuti: “Inu mukudziwa bwino za mawu amene Yehova analankhula+ kwa Mose munthu wa Mulungu woona,+ onena za ine ndi inu ku Kadesi-barinea.+  Ndinali ndi zaka 40 pamene Mose mtumiki wa Yehova anandituma kukazonda dziko,+ kuchokera ku Kadesi-barinea. Nditabwerako ndinamuuza kuchokera pansi pa mtima wanga, zonse zimene ndinaona.+  Anthu amene ndinapita nawo, anapangitsa mitima ya anthu kuchita mantha kwambiri.+ Koma ine ndinatsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.+  Chotero Mose anandilumbirira tsiku limenelo kuti, ‘Dziko limene wakaliponda ndi mapazi ako+ lidzakhala cholowa chako ndi cha ana ako mpaka kalekale, chifukwa watsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wako wonse.’+ 10  Yehova wandisunga ndi moyo+ monga mmene analonjezera.+ Tsopano padutsa zaka 45 kuchokera pamene Yehova analonjeza Mose, pa nthawi imene Aisiraeli anali m’chipululu,+ ndipo lero ndili ndi zaka 85. 11  Komabe ndikadali ndi mphamvu monga ndinalili pa tsiku limene Mose anandituma.+ Mmene mphamvu zanga zinalili pa nthawiyo, ndi mmenenso zilili panopa, moti ndikhoza kupita kunkhondo ndi kubwerako.+ 12  Choncho, ndipatseni dera lamapiri ili limene Yehova anandilonjeza pa tsiku lija.+ Pa tsikulo, ngakhale inuyo munamva kuti kumeneko kuli Aanaki+ ndi mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Koma mosakayikira Yehova akakhala nane,+ ndipo ndikawapitikitsa ndithu monga mmene Yehova analonjezera.”+ 13  Pamenepo Yoswa anadalitsa Kalebe mwana wa Yefune, ndi kum’patsa mzinda wa Heburoni monga cholowa chake.+ 14  N’chifukwa chake mzinda wa Heburoni uli cholowa cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi, kufikira lero. Anam’patsa mzindawo chifukwa iye anatsatira Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+ 15  Zimenezi zisanachitike, mzinda wa Heburoni unkatchedwa Kiriyati-ariba+ (Ariba+ anali munthu wamphamvu pakati pa Aanaki). Ndipo dziko lonse linakhala bata, lopanda nkhondo.+

Mawu a M'munsi