Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yoswa 12:1-24

12  Tsopano awa ndi mafumu amene ana a Isiraeli anagonjetsa n’kulanda madera awo, kumbali yotulukira dzuwa+ ya mtsinje wa Yorodano. Analanda kuchokera kuchigwa* cha Arinoni+ kukafika kuphiri la Herimoni+ ndi ku Araba+ konse, kumbali yotulukira dzuwa. Mafumu ake ndi awa:  Sihoni+ mfumu ya Aamori, yemwe ankakhala ku Hesiboni.+ Dera lomwe anali kulamulira linkayambira pakatikati pa chigwa cha Arinoni kuphatikizapo mzinda wa Aroweli,+ umene unali m’mphepete mwa mtsinje wa Arinoni,+ mpaka hafu ya Giliyadi kukalekezera kuchigwa cha Yaboki,+ kumalire ndi ana a Amoni.  Anali kulamuliranso chigwa cha Araba+ mpaka kunyanja ya Kinereti+ kumbali ya kum’mawa kwa nyanjayi, n’kukafikanso kunyanja ya Araba, yomwe ndi Nyanja Yamchere.+ Anali kulamulira kumbali ya kum’mawa kwa nyanjayi, cha ku Beti-yesimoti,+ mpaka kum’mwera, kumunsi kwa Pisiga.+  Mfumu ina ndi Ogi+ wa ku Basana yemwe anali mmodzi mwa Arefai+ otsala, ndipo ankakhala ku Asitaroti+ ndi ku Edirei.+  Anali kulamulira kuphiri la Herimoni,+ ku Saleka, ndi ku Basana+ konse, mpaka kukafika kumalire a Agesuri+ ndi Amaakati.+ Anali kulamuliranso hafu ya Giliyadi, mpaka kumalire ndi dera limene Sihoni,+ mfumu ya Hesiboni,+ anali kulamulira.  Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Isiraeli ndiwo anagonjetsa mafumuwa.+ Atatero, Mose mtumiki wa Yehova anapereka dzikoli kwa Arubeni,+ Agadi,+ ndi hafu ya fuko la Manase,+ kuti likhale lawo.  Yoswa ndi ana a Isiraeli anagonjetsa mafumu a kudera la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera ku Baala-gadi+ kuchigwa cha Lebanoni+ mpaka kuphiri la Halaki,+ limene lili moyang’anizana ndi Seiri.+ Atawagonjetsa, Yoswa anapereka dzikolo kwa mafuko a Isiraeli poligawa m’magawomagawo.+  Dzikoli linkaphatikizapo dera lamapiri, dera la Sefela, chigwa cha Araba, malo otsetsereka, chipululu, ndi Negebu.+ Limeneli linali dziko la Ahiti, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi.+ Mafumu awo anali awa:  Mfumu ya Yeriko,+ imodzi. Mfumu ya Ai+ pafupi ndi Beteli, imodzi. 10  Mfumu ya Yerusalemu,+ imodzi. Mfumu ya Heburoni,+ imodzi. 11  Mfumu ya Yarimuti,+ imodzi. Mfumu ya Lakisi,+ imodzi. 12  Mfumu ya Egiloni,+ imodzi. Mfumu ya Gezeri,+ imodzi. 13  Mfumu ya Debiri,+ imodzi. Mfumu ya Gederi, imodzi. 14  Mfumu ya Horima, imodzi. Mfumu ya Aradi, imodzi. 15  Mfumu ya Libina,+ imodzi. Mfumu ya Adulamu, imodzi. 16  Mfumu ya Makeda,+ imodzi. Mfumu ya Beteli,+ imodzi. 17  Mfumu ya Tapuwa, imodzi. Mfumu ya Heferi,+ imodzi. 18  Mfumu ya Afeki, imodzi. Mfumu ya Lasaroni, imodzi. 19  Mfumu ya Madoni,+ imodzi. Mfumu ya Hazori,+ imodzi. 20  Mfumu ya Simironi-meroni, imodzi. Mfumu ya Akasafu,+ imodzi. 21  Mfumu ya Taanaki, imodzi. Mfumu ya Megido,+ imodzi. 22  Mfumu ya Kadesi, imodzi. Mfumu ya Yokineamu+ ku Karimeli, imodzi. 23  Mfumu ya Dori kumapiri a Dori,+ imodzi. Mfumu ya Goimu ku Giligala, imodzi. 24  Mfumu ya Tiriza, imodzi. Mafumu onse analipo 31.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi a pa Ge 26:17.