Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yoswa 11:1-23

11  Ndiyeno Yabini mfumu ya ku Hazori+ atangomva nkhaniyi, anatumiza uthenga woitanitsa Yobabi mfumu ya ku Madoni, ndi mfumu ya ku Simironi, ndiponso mfumu ya ku Akasafu.+  Anatumizanso uthenga kwa mafumu amene anali m’dera lamapiri kumpoto, ndiponso m’chipululu kum’mwera kwa nyanja ya Kinereti,*+ mafumu a ku Sefela,+ ndiponso kwa mafumu okhala m’mapiri a Dori+ kumadzulo.  Anaitanitsanso Akanani+ okhala kum’mawa ndi kumadzulo, ndiponso Aamori,+ Ahiti,+ Aperezi+ ndi Ayebusi+ okhala kudera lamapiri. Komanso anaitanitsa Ahivi+ omwe anali kukhala m’munsi mwa phiri la Herimoni+ ku Mizipa.+  Choncho mafumuwo pamodzi ndi magulu awo onse ankhondo ananyamuka. Anali anthu ambiri, kuchuluka kwawo ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.+ Ndipo anali ndi mahatchi*+ ambiri zedi komanso magaleta* ankhondo.  Mafumu onsewa anakumana pamodzi monga anapanganirana. Ndiyeno onse pamodzi anakamanga msasa pafupi ndi madzi a ku Meromu kuti akamenyane ndi Aisiraeli.+  Pamenepo Yehova anauza Yoswa kuti: “Usawaope,+ pakuti mawa pa nthawi ngati yomwe ino, ndidzawapereka onsewo kuti aphedwe ndi Aisiraeli. Mahatchi awo udzawapundula,*+ ndipo magaleta awo udzawatentha ndi moto.”+  Yoswa ndi asilikali ake onse anapita kufupi ndi madzi a Meromu ndi kuthira nkhondo adaniwo modzidzimutsa.  Ndipo Yehova anapereka adaniwo m’manja mwa Aisiraeli.+ Chotero anayamba kuwapha ndi kuwathamangitsa mpaka kukafika kumzinda wa anthu ambiri wa Sidoni,+ ku Misirepotu-maimu+ ndi kuchigwa cha Mizipe+ kum’mawa. Anapitiriza kuwapha moti panalibe amene anapulumuka.+  Pambuyo pake Yoswa anachita zimene Yehova anamuuza. Mahatchi awo anawapundula,+ ndipo magaleta awo anawatentha ndi moto.+ 10  Kuwonjezera apo, Yoswa anabwerera ndi kukalanda+ mzinda wa Hazori+ n’kupha mfumu yake ndi lupanga.+ Anachita zimenezi chifukwa mzinda wa Hazori unali likulu la maufumu onsewa. 11  Aisiraeliwo anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mumzindawo.+ Panalibe chamoyo chilichonse chimene chinatsala,+ ndipo Yoswa anatentha mzinda wa Hazori ndi moto. 12  Yoswa analanda mizinda yonse ya mafumuwa, ndi kugwira mafumu onse a mizindayi n’kuwapha ndi lupanga.+ Anawawononga onsewo+ monga mmene analamulira Mose mtumiki wa Yehova.+ 13  Mizinda yonse imene inamangidwa pamabwinja a mizinda yakale, Aisiraeli sanaitenthe ndi moto, kupatulapo mzinda wa Hazori umene Yoswa anautentha ndi moto. 14  Ana a Isiraeli anafunkha katundu yense wa m’mizindayi ndi ziweto zomwe.+ Koma anthu anawapha ndi lupanga kufikira atawamaliza onse.+ Sanasiye munthu aliyense wamoyo.+ 15  Monga Yehova analamulira mtumiki wake Mose, nayenso Mose analamula Yoswa,+ ndipo Yoswayo anachitadi zimenezo. Palibe mawu alionse amene Yoswa anasiya pa mawu onse amene Yehova analamula Mose.+ 16  Yoswa analanda dziko lonselo, dera lamapiri, dera lonse la Negebu,+ dziko lonse la Goseni,+ ku Sefela,+ ku Araba+ ndiponso dera lamapiri la Isiraeli ndi zigwa zake.+ 17  Analandanso dera lochokera kuphiri la Halaki+ lomwe lili moyang’anizana ndi Seiri+ mpaka kukafika ku Baala-gadi,+ kuchigwa cha Lebanoni m’munsi mwa phiri la Herimoni.+ Yoswa anagwira mafumu awo onse ndi kuwapha.+ 18  Iye anachita nkhondo ndi mafumu onsewa kwa masiku ambiri. 19  Panalibe mzinda winanso umene unapangana za mtendere ndi ana a Isiraeli kupatulapo Ahivi+ okhala mumzinda wa Gibeoni.+ Ana a Isiraeli analanda mizinda ina yonse mwankhondo.+ 20  Yehova analola mitunduyo kuumitsa mitima+ yawo kuti ichite nkhondo ndi Aisiraeli. Anatero kuti iye awawononge ndi kuti Aisiraeliwo asawamvere chisoni,+ koma kuti awatheretu monga mmene Yehova analamulira Mose.+ 21  Kuwonjezera apo, pa nthawiyo Yoswa anapita n’kukafafaniziratu Aanaki.+ Aanakiwo anali kukhala kudera lamapiri, ku Heburoni, ku Debiri, ku Anabi,+ kudera lonse lamapiri la Yuda ndiponso kudera lonse lamapiri la Isiraeli.+ Yoswa anafafaniziratu Aanakiwo pamodzi ndi mizinda yawo.+ 22  M’dziko la ana a Isiraeli, palibe Aanaki amene anatsalamo,+ kupatulapo okhala ku Gaza,+ ku Gati+ ndi ku Asidodi.+ 23  Chotero Yoswa analanda dziko lonse monga mmene Yehova analonjezera Mose.+ Ndiyeno Yoswa anapereka dzikolo kwa Aisiraeli monga cholowa chawo, malinga ndi magawo awo potsata mafuko awo.+ Ndipo dziko lonse linakhala bata, lopanda nkhondo.+

Mawu a M'munsi

M’Baibulo, “nyanja ya Kinereti” imatchulidwanso ndi mayina akuti, “nyanja ya Genesarete,” “nyanja ya Galileya” komanso “nyanja ya Tiberiyo.”
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Anali ‘kuwapundula’ mwa kudula mtsempha wakuseri kwa mwendo wakumbuyo.