Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yona 3:1-10

3  Yehova analankhula ndi Yona kachiwiri kuti:+  “Nyamuka, upite kumzinda waukulu wa Nineve, ndipo kumeneko ukalalikire+ zimene ndikuuze.”  Pamenepo Yona ananyamuka ndi kupita ku Nineve mogwirizana ndi mawu a Yehova.+ Mzinda wa Nineve unali waukulu pamaso pa Mulungu, ndipo mtunda wake unali woyenda masiku atatu.  Kenako Yona analowa mumzindawo ndi kuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye anali kulalikira kuti: “Kwangotsala masiku 40 okha ndipo Nineve awonongedwa.”+  Anthu a ku Nineve anayamba kukhulupirira Mulungu ndipo anayamba kulengeza kuti aliyense, popanda wotsala, asale kudya ndipo avale ziguduli.*  Uthengawo utafika kwa mfumu ya Nineve,+ mfumuyo inanyamuka pampando wake wachifumu ndi kuvula chovala chake chachifumu. Ndiyeno inavala chiguduli ndi kukhala paphulusa.+  Kuwonjezera pamenepo, mfumu ndi akuluakulu ake analamula anthu kuti alengeze mu Nineve kuti: “Munthu aliyense, chiweto, ng’ombe ndi nkhosa iliyonse zisadye chilichonse. Munthu aliyense kapena chiweto zisadye chakudya kapena kumwa madzi.  Munthu aliyense komanso ziweto zivale chiguduli. Afuulire Mulungu ndi mphamvu zawo zonse, ndipo aliyense asiye njira zake zoipa+ ndi zinthu zonse zachiwawa zimene amachita.  Ndani angadziwe? Mwina Mulungu woona satigwetsera tsoka ndipo asintha maganizo+ ndi kubweza mkwiyo wake woyaka moto, moti satiwononga.”+ 10  Ndiyeno Mulungu woona anaona ntchito zawo. Anaona kuti alapa ndi kusiya njira zawo zoipa.+ Choncho, Mulungu woona anasintha maganizo ake+ pa tsoka limene ananena kuti awabweretsera, moti sanawabweretsere.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masaka.”