Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yona 2:1-10

2  Tsopano Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake, ali m’mimba mwa chinsombacho,+  kuti: “Pamene ndinali m’masautso ndinaitana Yehova,+ ndipo anandiyankha.+ Ndinafuula kupempha thandizo ndili m’Manda* akuya.+ Ndipo inu munamva mawu anga.+   Pamene munandiponya m’malo ozama, pansi penipeni pa nyanja yakuya,+ Madzi amphamvu anandimiza. Mafunde anu amphamvu anadutsa pamwamba panga.+   Ndipo ine ndinati, ‘Mwandipitikitsa pamaso panu!+ Kodi kachisi wanu woyera ndidzamuonanso?’+   Ndinatsala pang’ono kufa+ chifukwa madzi anandimiza. Zomera zam’nyanja zinakulunga mutu wanga.   Ndinatsikira m’tsinde mwenimweni mwa mapiri. Zotsekera za dziko lapansi zinanditsekereza kuti ndikhale komweko mpaka kalekale.* Koma inu Yehova Mulungu wanga, munanditulutsa m’dzenje ndili wamoyo.+   Pamene ndinalefuka kwambiri,+ ndinakumbukira Yehova.+ Ndipo pemphero langa linafika kwa inu, m’kachisi wanu woyera.+   Anthu okhulupirira mafano, amaleka kusonyeza kukoma mtima kwawo kosatha.+   Koma ine, ndidzakutamandani ndi kupereka nsembe kwa inu.+ Zimene ndalonjeza ndidzazikwaniritsa.+ Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”+ 10  Kenako Yehova analamula chinsombacho, ndipo chinalavula Yona kumtunda.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 5.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.