Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yohane 17:1-26

17  Yesu atalankhula zinthu zimenezi, anakweza maso ake kumwamba+ ndi kunena kuti: “Atate, nthawi yafika, lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni.+  Inu mwamupatsa ulamuliro pa anthu onse,+ kuti onse amene inu mwamupatsa,+ awapatse moyo wosatha.+  Pakuti moyo wosatha+ adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa+ za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona,+ ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.+  Ndakulemekezani+ padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa.+  Ndipo tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.+  “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu.+ Anali anu, koma munawapereka kwa ine, ndipo iwo asunga mawu anu.  Tsopano adziwa kuti zonse zimene munandipatsa n’zochokera kwa inu,  chifukwa mawu amene munandipatsa ndawapereka kwa iwo.+ Iwo awalandira ndipo adziwa ndithu kuti ine ndinabwera monga nthumwi yanu,+ ndipo akhulupirira kuti ndinu amene munandituma.+  Choncho ndikupempha m’malo mwa iwo, sindikupemphera dziko,+ koma awo amene mwandipatsa, chifukwa iwo ndi anu. 10  Zonse zimene ndili nazo ndi zanu ndipo zanu zonse ndi zanga.+ Ine ndalemekezeka pakati pawo. 11  “Komanso, ine sindikhalanso m’dzikoli pakuti ndikubwera kwa inu, koma iwo adakali m’dzikoli.+ Atate Woyera, ayang’anireni+ chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa, kuti akhale amodzi mmene ife tilili.+ 12  Pamene ndinali nawo pamodzi, ndinali kuwayang’anira+ chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa. Ine ndawasunga moti palibe aliyense wa iwo amene wawonongeka+ kupatulapo mwana wa chiwonongeko,+ kuti malemba akwaniritsidwe.+ 13  Koma tsopano ndikubwera kwa inu, ndipo ndikulankhula zimenezi pamene ndili m’dziko kuti akhale ndi chimwemwe chosefukira ngati chimene ine ndili nacho.+ 14  Iwo ndawapatsa mawu anu, koma dziko likudana nawo,+ chifukwa sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.+ 15  “Sindikupempha kuti muwachotse m’dziko, koma kuti muwayang’anire kuopera woipayo.+ 16  Iwo sali mbali ya dziko,+ monganso ine sindili mbali ya dziko.+ 17  Ayeretseni+ ndi choonadi. Mawu+ anu ndiwo choonadi.+ 18  Monga mmene munanditumizira ine m’dziko, inenso ndawatumiza m’dziko.+ 19  Ndipo ine ndikudziyeretsa chifukwa cha iwo, kuti iwonso ayeretsedwe+ ndi choonadi. 20  “Sindikupemphera awa okha, komanso amene amakhulupirira ine kudzera m’mawu awo,+ 21  kuti onsewa akhale amodzi,+ mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana,+ kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife,+ ndi kuti dziko likhulupirire kuti inu munanditumadi.+ 22  Komanso, ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa, kuti iwo akhale amodzi mmene ifenso tilili amodzi.+ 23  Ine wogwirizana ndi iwo, inu wogwirizana ndi ine, kuti iwo akhale mu umodzi weniweni,+ kuti dziko lidziwe kuti inu munandituma ine, ndi kuti munawakonda iwo mmene munandikondera ine. 24  Atate, ine ndikufuna kuti amene mwandipatsawa adzakhale limodzi ndi ine kumene ine ndidzakhale,+ kuti adzaone ulemerero wanga umene inu mwandipatsa, chifukwa munandikonda musanayale maziko+ a dziko.+ 25  Atate wolungama,+ ndithudi dziko silinakudziweni,+ koma ine ndikukudziwani ndipo awa adziwa kuti inu munandituma.+ 26  Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu+ ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”+

Mawu a M'munsi