Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yohane 15:1-27

15  “Ine ndine mtengo wa mpesa weniweni,+ ndipo Atate wanga ndiye mlimi.+  Nthambi iliyonse mwa ine yosabala zipatso amaidula,+ ndipo iliyonse yobala zipatso amaiyeretsa mwa kuitengulira+ kuti ibale zipatso zambiri.+  Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ine ndalankhula kwa inu.+  Khalani ogwirizana ndi ine, inenso ndikhala wogwirizana ndi inu.+ Nthambi singabale zipatso payokha, pokhapokha ngati ndi yolumikizikabe kumpesawo. Chimodzimodzi inunso, simungabale zipatso mukapanda kukhala olumikizika kwa ine.+  Ine ndine mtengo wa mpesa, inu ndinu nthambi zake. Amene ali wolumikizika kwa ine, inenso n’kukhala wolumikizika kwa iye, ameneyo amabala zipatso zochuluka,+ chifukwa simungathe kuchita kalikonse popanda ine.  Ngati munthu sakhala wolumikizika kwa ine, amaponyedwa kunja monga nthambi ndipo amauma. Nthambi zoterozo anthu amazisonkhanitsa ndi kuziponya pamoto ndipo zimapsa.+  Ngati mukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.+  Atate amalemekezeka mukapitiriza kubala zipatso zambiri ndi kusonyeza kuti mulidi ophunzira anga.+  Monga Atate wakondera ine,+ inenso kukonda inu, inunso khalanibe m’chikondi changa. 10  Mukasunga malamulo anga,+ mudzakhalabe m’chikondi changa, monga mmene ine ndasungira malamulo a Atate+ ndi kukhalabe m’chikondi chake. 11  “Ndalankhula zinthu izi kwa inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chisefukire.+ 12  Lamulo langa ndi ili, mukondane monga mmene inenso ndakukonderani.+ 13  Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.+ 14  Mupitiriza kukhala mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.+ 15  Sindikutchanso inu kuti akapolo, chifukwa kapolo sadziwa zimene mbuye wake amachita. Koma ndakutchani mabwenzi,+ chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.+ 16  Inu simunandisankhe ine, koma ine ndinakusankhani. Ndinakuikani kuti mupitirize kubala zipatso zochuluka,+ ndi kutinso zipatso zanuzo zisathe, kuti chilichonse chimene mungapemphe Atate m’dzina langa akupatseni.+ 17  “Ndikukulamulani zinthu izi, kuti muzikondana.+ 18  Ngati dziko likudana nanu, mukudziwa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu.+ 19  Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake.+ Koma popeza simuli mbali ya dzikoli,+ koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.+ 20  Kumbukirani mawu amene ndinakuuzani aja, kapolo sali wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.+ Ngati asunga mawu anga, adzasunganso anu. 21  Koma adzakuchitirani zonsezi chifukwa cha dzina langa, chifukwa amene anandituma ine sakumudziwa.+ 22  Ndikanapanda kubwera kudzalankhula nawo, akanakhala opanda tchimo,+ koma tsopano alibe chodzilungamitsira pa tchimo lawo.+ 23  Wodana ndi ine amadananso ndi Atate wanga.+ 24  Ndikanapanda kuchita pakati pawo ntchito zimene wina aliyense sanachitepo,+ akanakhala opanda tchimo,+ koma tsopano aona ndipo adana nane, ndi kudananso ndi Atate wanga.+ 25  Zili choncho kuti mawu olembedwa m’Chilamulo akwaniritsidwe. Mawu ake ndi akuti, ‘Anadana nane popanda chifukwa.’+ 26  Akadzafika mthandizi amene ndidzamutumiza kuchokera kwa Atate,+ amene ndi mzimu wa choonadi wochokera kwa Atate, ameneyo adzandichitira umboni,+ 27  ndipo inunso mudzachitira umboni,+ chifukwa mwakhala nane kuchokera pa chiyambi.

Mawu a M'munsi