Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yohane 13:1-38

13  Tsopano Yesu anadziwiratu chikondwerero cha pasika chisanafike, kuti nthawi yake yochoka m’dzikoli kupita kwa Atate+ yakwana.+ Ndipo popeza kuti anali kuwakonda akewo amene anali m’dzikoli,+ anawakonda mpaka pa mapeto a moyo wake.  Chakudya chamadzulo chili mkati, Mdyerekezi anali ataika kale maganizo ofuna kupereka Yesu+ mumtima mwa Yudasi Isikariyoti,+ mwana wa Simoni.  Yesu anali kudziwa kuti Atate anapereka zinthu zonse m’manja mwake.+ Analinso kudziwa kuti anabwera kuchokera kwa Mulungu ndi kuti anali kupita kwa Mulungu.+  Choncho anaimirira pa chakudya chamadzulocho ndi kuvula malaya ake akunja. Kenako anatenga thaulo ndi kumanga m’chiuno mwake.+  Atatero anathira madzi m’beseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi+ a ophunzira ndi kuwapukuta ndi thaulo limene anamanga m’chiuno lija.  Kenako anafika pa Simoni Petulo. Koma Petulo anauza Yesu kuti: “Ambuye, inuyo mukufuna musambitse mapazi anga?”+  Yesu anayankha kuti: “Zimene ndikuchitazi sungazimvetse padakali pano, koma pambuyo pake udzamvetsa.”+  Petulo anati: “Ndithu, sizitheka kuti inu musambitse mapazi anga.” Yesu anamuyankha kuti: “Ndikapanda kukusambitsa,+ palibe chako kwa ine.”  Simoni Petulo anati: “Ambuye, musandisambitse mapazi okha, komanso manja ndi mutu womwe.” 10  Yesu anati: “Amene wasamba m’thupi+ amangofunika kusamba mapazi okha basi, chifukwa thupi lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, koma osati nonsenu.” 11  Iye anadziwa ndithu za munthu amene wakonza zomupereka.+ N’chifukwa chake ananena kuti: “Sikuti nonsenu ndinu oyera ayi.” 12  Tsopano atasambitsa mapazi awo ndi kuvalanso malaya ake akunja aja, anakhalanso patebulo. Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi mukudziwa zimene ndachita kwa inu? 13  Inu mumanditcha kuti ‘Mphunzitsi’+ ndi ‘Ambuye,’+ mumalondola, pakuti ndinedi.+ 14  Choncho ngati ine, wokhala Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu,+ inunso muyenera kusambitsana mapazi.+ 15  Pakuti ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.+ 16  Ndithudi ndikukuuzani, Kapolo saposa mbuye wake, ndiponso wotumidwa saposa amene wamutuma.+ 17  Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.+ 18  Sindikunena nonsenu, ndikudziwa amene ndawasankha.+ Koma zili choncho kuti Malemba akwaniritsidwe,+ paja amati, ‘Munthu amene anali kudya chakudya changa wanyamula chidendene chake kundiukira.’+ 19  Kuyambira tsopano ndikukuuziranitu zisanachitike,+ kuti zikadzachitika mudzakhulupirire kuti ine ndinedi amene munali kumuyembekezera uja. 20  Ndithudi ndikukuuzani, Wolandira aliyense amene ine ndamutuma walandiranso ine.+ Ndipo amene walandira ine, walandiranso amene anandituma.”+ 21  Atanena zimenezi, Yesu anasautsika mu mzimu, ndipo anachitira umboni kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mmodzi wa inu andipereka.”+ 22  Ophunzirawo anayamba kuyang’anizana posadziwa kuti anali kunena ndani.+ 23  Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anali kumukonda,+ anakhala patsogolo pa Yesu, pachifuwa chake. 24  Chotero Simoni Petulo anamukodola ndi mutu ndi kumuuza kuti: “Tiuze kuti akunena ndani.” 25  Pamenepo winayo anatsamira pachifuwa pa Yesu ndi kumufunsa kuti: “Ambuye, mukunena ndani?”+ 26  Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndimupatse chidutswa cha mkate chimene ndisunse.”+ Choncho atasunsa chidutswa cha mkate chija, anapatsa Yudasi, mwana wa Simoni Isikariyoti. 27  Atamupatsa chidutswa cha mkatecho, pamenepo Satana analowa mwa Yudasi.+ Chotero Yesu anamuuza kuti: “Zimene wakonza kuchita, zichite mwamsanga.” 28  Koma panalibe aliyense mwa okhala patebulowo amene anadziwa chifukwa chimene anamuuzira zimenezi. 29  Popeza kuti Yudasi anali kusunga bokosi la ndalama,+ ena anali kuganiza kuti Yesu anali kumuuza kuti: “Ugule zofunikira zonse za chikondwerero,” kapena kuti apereke kenakake kwa osauka.+ 30  Choncho atalandira chidutswa cha mkate chija, anatuluka nthawi yomweyo. Umenewu unali usiku.+ 31  Yudasi atatuluka, Yesu anati: “Tsopano Mwana wa munthu walemekezedwa,+ ndipo Mulungu walemekezedwa kudzera mwa iye. 32  Mulungunso payekha amulemekeza iye,+ ndipo amulemekeza nthawi yomwe ino. 33  Ana apamtima inu,+ ndikhala nanu kanthawi kochepa chabe. Mudzandifunafuna, ndipo monga ndinauzira Ayuda aja kuti, ‘Kumene ine ndikupita simungathe kukafikako,’+ tsopano ndikuuzanso inuyo. 34  Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani,+ inunso muzikondana.+ 35  Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”+ 36  Simoni Petulo anafunsa kuti: “Ambuye, mukupita kuti?” Yesu anayankha kuti: “Kumene ndikupita sunganditsatire padakali pano, koma udzanditsatira m’tsogolo.”+ 37  Petulo anafunsanso kuti: “Ambuye, n’chifukwa chiyani sindingakutsatireni padakali pano? Ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha inu.”+ 38  Yesu anayankha kuti: “Kodi udzapereka moyo wako chifukwa cha ine? Ndithudi ndikukuuza iwe, Tambala asanalire undikana katatu.”+

Mawu a M'munsi