Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yohane 10:1-42

10  “Ndithudi ndikukuuzani, Wolowa m’khola la nkhosa mochita kukwera pamalo ena osati kudzera pakhomo,+ ameneyo ndi wakuba ndiponso wofunkha.+  Koma wolowera pakhomo,+ ameneyo ndiye m’busa+ wa nkhosazo.+  Mlonda wa pakhomo+ amamutsegulira ameneyu, ndipo nkhosa+ zimamvera mawu ake. Nkhosa zakezo amazitchula mayina ndi kuzitsogolera kutuluka nazo.  Akatulutsa zake zonse kunja, amazitsogolera, ndipo nkhosazo zimamutsatira,+ chifukwa zimadziwa mawu ake.+  Mlendo sizidzamutsatira ayi koma zidzamuthawa,+ chifukwa sizidziwa mawu a alendo.”+  Yesu ananena fanizoli kwa iwo, koma iwo sanadziwe tanthauzo la zinthu zimene anali kuwauzazo.+  Choncho Yesu anawauzanso kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Ine ndine khomo+ la nkhosa.  Onse amene abwera m’malo mwa ine ndi akuba ndiponso ofunkha,+ ndipo nkhosa sizinawamvere.+  Ine ndine khomo.+ Aliyense wolowa kudzera mwa ine adzapulumuka, ndipo azidzalowa ndi kutuluka, kukapeza msipu.+ 10  Wakuba+ sabwera ndi cholinga china ayi, koma kudzaba, kudzapha ndi kudzawononga.+ Koma ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, inde kuti akhale nawo wochuluka. 11  Ine ndine m’busa wabwino.+ M’busa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.+ 12  Munthu waganyu,+ amene si m’busa ndipo nkhosazo si zake, akaona mmbulu ukubwera amasiya nkhosazo ndi kuthawa, pamenepo mmbuluwo umazigwira ndi kuzibalalitsa,+ 13  chifukwa iye ndi waganyu+ chabe, ndipo sasamala za nkhosazo.+ 14  Ine ndine m’busa wabwino, nkhosa zanga ndimazidziwa,+ izonso zimandidziwa,+ 15  monga mmene zilili kuti Atate amandidziwa, inenso ndimawadziwa Atate.+ Chotero, ndipereka moyo wanga chifukwa cha nkhosazo.+ 16  “Ndili ndi nkhosa zina+ zimene sizili za khola ili,+ zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga,+ ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.+ 17  Chimene Atate amandikondera n’chakuti,+ ndikupereka moyo wanga+ kuti ndikaulandirenso. 18  Palibe munthu amene akuuchotsa kwa ine, koma ndikuupereka mwa kufuna kwanga. Ndili ndi mphamvu zoupereka, ndiponso ndili ndi mphamvu zoulandiranso.+ Atate wanga ndi amene anandilamula+ kuchita zimenezi.” 19  Apanso panakhala kugawanika+ maganizo pakati pa Ayuda chifukwa cha mawu amenewa. 20  Ambiri a iwo anali kunena kuti: “Ameneyu ali ndi chiwanda+ ndipo ndi wamisala. N’chifukwa chiyani mukumumvetsera?” 21  Ena anali kunena kuti: “Amenewa si mawu a munthu wogwidwa ndi chiwanda ayi. Kodi chiwanda chingatsegule maso a anthu akhungu?” 22  Pa nthawiyo mu Yerusalemu munachitika chikondwerero cha kupereka kachisi kwa Mulungu. Inali nyengo ya chisanu, 23  ndipo Yesu anali kuyenda m’kachisimo, m’khonde la zipilala la Solomo.+ 24  Choncho Ayuda anamuzungulira ndi kuyamba kumuuza kuti: “Utivutitsa maganizo mpaka liti? Ngati ndiwedi Khristu,+ tiuze mosapita m’mbali.”+ 25  Yesu anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale, koma inu simukukhulupirira. Ntchito zimene ine ndikuchita m’dzina la Atate wanga, zikundichitira umboni.+ 26  Koma inu simukukhulupirira, chifukwa si inu nkhosa zanga.+ 27  Nkhosa+ zanga zimamva mawu anga. Ine ndimazidziwa, ndipo izo zimanditsatira.+ 28  Ndidzazipatsa moyo wosatha,+ moti sizidzawonongeka,+ komanso palibe amene adzazitsomphole m’dzanja langa.+ 29  Chimene Atate+ wanga wandipatsa n’chofunika kuposa zinthu zonse,+ ndipo palibe amene angazitsomphole m’dzanja la Atate.+ 30  Ine ndi Atate ndife amodzi.”+ 31  Apanso Ayudawo anatola miyala kuti amugende.+ 32  Yesu anawauza kuti: “Ndakuonetsani ntchito zambiri zabwino zochokera kwa Atate. Tsopano mukundiponya miyala chifukwa cha ntchito iti mwa zimenezi?” 33  Ayudawo anamuyankha kuti: “Sitikukuponya miyala chifukwa cha ntchito yabwino ayi, koma chifukwa chonyoza Mulungu.+ Iwe ndiwe munthu wamba koma ukudziyesa mulungu.”+ 34  Yesu anawafunsa kuti: “Kodi m’Chilamulo chanu sanalembemo+ kuti, ‘Ine ndinati: “Inu ndinu milungu”’?+ 35  Ngati anthu amene anatsutsidwa ndi mawu a Mulungu anawatcha ‘milungu,’+ ndipo Malemba satha mphamvu,+ 36  nanga kodi inu mukundiuza ine woyeretsedwa ndi Atate ndi kutumizidwa m’dziko kuti, ‘Ukunyoza Mulungu,’ chifukwa ndanena kuti, Ndine Mwana wa Mulungu?+ 37  Ngati sindikuchita ntchito+ za Atate wanga, musandikhulupirire. 38  Koma ngati ndikuzichita, ngakhale simukundikhulupirira, khulupirirani ntchitozo,+ kuti mudziwe ndi kupitirizabe kudziwa kuti Atate ndi ine ndife ogwirizana.”+ 39  Pamenepo anayesanso kumugwira,+ koma anawazemba.+ 40  Chotero anawolokanso Yorodano ndi kupita kumene Yohane anali kubatizira+ poyamba, ndipo anakhala kumeneko. 41  Anthu ambiri anabwera kwa iye, ndi kuyamba kunena kuti: “Yohane sanachite chizindikiro chilichonse, koma zonse zimene Yohane ananena zokhudza munthu uyu zinali zoona.”+ 42  Choncho anthu ambiri kumeneko anamukhulupirira.+

Mawu a M'munsi