Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yohane 1:1-51

1  Pa chiyambi,+ panali wina wotchedwa Mawu,+ ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu,+ komanso Mawuyo anali mulungu.*+  Ameneyu anali ndi Mulungu+ pa chiyambi.+  Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye,+ ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.   Moyo unakhalapo kudzera mwa iye,+ ndipo moyowo unali kuwala+ kounikira anthu.  Kuwalako kukuunika mumdima,+ ndipo mdimawo sunagonjetse kuwalako.  Panaonekera munthu wina amene anatumidwa monga nthumwi ya Mulungu.+ Dzina lake anali Yohane.+  Munthu ameneyu anabwera monga mboni,+ kudzachitira umboni za kuwala,+ kuti anthu osiyanasiyana akhulupirire kudzera mwa iye.+  Sikuti iyeyu anali kuwalako ayi,+ koma anangobwera kudzachitira umboni+ za kuwalako.  Kuwala+ kwenikweni kumene kumaunikira+ anthu osiyanasiyana+ kunali pafupi kubwera m’dziko. 10  Iye anali m’dziko,+ ndipo dziko linakhalapo kudzera mwa iye.+ Koma dzikolo silinamudziwe. 11  Anabwera kudziko lakwawo, koma anthu akwawo enieniwo sanamulandire.+ 12  Komabe onse amene anamulandira,+ anawapatsa mphamvu zokhala ana a Mulungu,+ chifukwa amenewa anakhulupirira m’dzina lake.+ 13  Iwowa anabadwa kwa Mulungu, osati kudzera m’magazi kapena m’chifuniro cha thupi, kapena chifuniro cha anthu.+ 14  Choncho Mawu ameneyo anakhala ndi thupi+ la nyama ndi kukhala pakati pathu, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wa mwana wobadwa yekha+ kwa bambo ake. Anali wodzaza ndi kukoma mtima kwakukulu ndi choonadi.+ 15  (Yohane anachitira umboni za iye, moti anali kuchita kufuula kuti: “Amene akubwera m’mbuyo mwangamu wandipitirira ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.”)+ 16  Pakuti tonsefe tinalandira zinthu kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo.+ Tinalandira kukoma mtima kwakukulu kosefukira.+ 17  Popeza Chilamulo chinaperekedwa kudzera mwa Mose,+ kukoma mtima kwakukulu+ komanso choonadi+ zinakhalako kudzera mwa Yesu Khristu. 18  Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse,+ mulungu wobadwa yekha+ amene ali pachifuwa+ cha Atate ndiye amene anafotokoza za Mulungu.+ 19  Tsopano, Yohane anapereka umboni pamene Ayuda anatumiza ansembe ndi Alevi kuchokera ku Yerusalemu kukamufunsa kuti: “Kodi iwe ndiwe ndani?”+ 20  Iye anavomereza osakana ayi. Anavomereza ndithu, kuti: “Ine sindine Khristu ayi.”+ 21  Iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Ndiwe Eliya kapena?”+ Koma iye anati: “Iyayi.” “Kapena ndiwe Mneneri?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi!” 22  Choncho iwo anamufunsa kuti: “Ndiwe ndani nanga? Tikufuna kudziwa kuti tikathe kupereka yankho kwa amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe ndani?”+ 23  Iye anati: “Ndine mawu a winawake wofuula m’chipululu kuti, ‘Wongolani njira ya Yehova,’ monga mmene mneneri Yesaya ananenera.”+ 24  Otumidwawo anachokera kwa Afarisi. 25  Choncho anamufunsa kuti: “Ngati iweyo sindiwe Khristu, kapena Eliya, kapenanso Mneneri, nanga n’chifukwa chiyani umabatiza anthu?”+ 26  Yohane anawayankha kuti: “Ine ndimabatiza m’madzi. Pakati panu+ paimirira wina amene inu simukumudziwa.+ 27  Iye ndiye amene akubwera m’mbuyo mwangamu. Komabe, zingwe za nsapato zake ine sindili woyenera kuzimasula.”+ 28  Izi zinachitikira ku Betaniya wa kutsidya lina la Yorodano, kumene Yohane anali kubatiza anthu.+ 29  Tsiku lotsatira anaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo anati: “Taonani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu amene akuchotsa uchimo+ wa dziko!+ 30  Uyu ndi amene ndinali kunena uja kuti, M’mbuyo mwanga mukubwera munthu wina amene wandipitirira ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.+ 31  Inenso sindinali kumudziwa, koma chimene ndikubatizira anthu m’madzi n’chakuti iyeyu aonekere kwa Isiraeli.”+ 32  Yohane anachitiranso umboni kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba, ndipo unakhalabe pa iye.+ 33  Inenso sindinali kumudziwa, koma Amene anandituma+ kudzabatiza m’madzi anandiuza kuti, ‘Ukadzaona mzimu ukutsika ndi kukhazikika pa munthu wina, ameneyo ndiye wobatiza ndi mzimu woyera.’+ 34  Ndipo ine ndaonadi zimenezo, ndachitira umboni ndithu kuti iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.”+ 35  Tsiku lotsatiranso Yohane anaimirira ndi ophunzira ake awiri. 36  Poyang’anitsitsa Yesu akuyenda iye anati: “Onani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu!” 37  Ophunzira awiriwo anamumva akulankhula, ndipo anatsatira Yesu. 38  Pamenepo Yesu anacheuka. Atawaona akumutsatira, anawafunsa kuti: “Kodi mukufunafuna chiyani?” Iwo anati: “Rabi, (dzina lotanthauza, Mphunzitsi, polimasulira,) kodi mukukhala kuti?” 39  Iye anati: “Tiyeni mukaoneko.”+ Choncho anapita ndi kukaona kumene anali kukhala, ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Pamenepo n’kuti nthawi ili cha m’ma 4 koloko madzulo.* 40  Andireya+ m’bale wake wa Simoni Petulo, anali mmodzi wa awiriwo amene anamva zimene Yohane ananena ndi kutsatira Yesu. 41  Choyamba iyeyu anapeza m’bale wake Simoni, ndi kumuuza kuti: “Ifetu tapeza Mesiya”+ (dzina lotanthauza, Khristu,+ polimasulira). 42  Kenako iye anapita naye kwa Yesu. Yesu atamuyang’ana+ anati: “Iwe ndiwe Simoni+ mwana wa Yohane,+ udzatchedwa Kefa” (dzina limene kumasulira kwake ndi Petulo).+ 43  Tsiku lotsatira, Yesu anaganiza zopita ku Galileya. Ndiyeno anapeza Filipo+ n’kumuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”+ 44  Filipo anali wochokera ku Betsaida,+ mumzinda wa Andireya ndi Petulo. 45  Kenako Filipo anapeza Natanayeli+ n’kumuuza kuti: “Uja amene Mose analemba za iye m’Chilamulo+ komanso wotchulidwa m’Zolemba za aneneri,+ ife tam’peza. Iyeyu ndi Yesu, mwana wa Yosefe,+ wa ku Nazareti.” 46  Koma Natanayeli anamufunsa kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?”+ Pamenepo Filipo anati: “Tiye ukaone.” 47  Yesu ataona Natanayeli akubwera momulunjika anati: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.”+ 48  Natanayeli anati: “Mwandidziwa bwanji?” Yesu anamuyankha kuti: “Filipo asanakuitane, ine ndinakuona, muja unali pansi pa mkuyu paja.” 49  Natanayeli anamuyankha kuti: “Rabi, ndinudi Mwana wa Mulungu,+ ndinu Mfumu+ ya Isiraeli.” 50  Poyankha Yesu anati: “Kodi wakhulupirira chifukwa ndakuuza kuti ndinakuona uli pansi pa mkuyu? Udzaona zazikulu kuposa izi.” 51  Anamuuzanso kuti: “Ndithudi ndikukuuzani anthu inu, mudzaona kumwamba kutatseguka, angelo+ a Mulungu akukwera ndi kutsikira kwa Mwana wa munthu.”+

Mawu a M'munsi

“Wonga mulungu, waumulungu.” Onani Zakumapeto 10.
Mawu ake enieni, “ola la 10,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.