Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 7:1-21

7  “Kodi si paja munthu amagwira ntchito yokakamiza+ padziko lapansi? Ndipo kodi masiku ake sali ngati masiku a munthu waganyu?+   Monga kapolo, iye amakhala wefuwefu kufunafuna mthunzi,+ Ndipo ngati munthu waganyu, amadikirira malipiro ake.+   Chotero ndalandira miyezi yachabechabe ngati cholowa,+ Ndipo kuvutika usiku uliwonse+ ndiwo malipiro anga.   Ndikagona ndimanena kuti, ‘Kodi ndidzuka nthawi yanji?’+ Kukada ndimangokhalira kutembenukatembenuka mpaka m’mawa kuli mbuu.   Mnofu wanga wakutidwa ndi mphutsi+ ndipo wamatirira fumbi,+ Khungu langa lang’ambika n’kumatuluka mafinya.+   Masiku anga akufulumira+ kuposa mmene chimathamangira chowombera nsalu, Iwo afika pamapeto popanda chiyembekezo.+   Kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mphepo,+ Ndiponso kuti diso langa silidzaonanso zabwino.   Diso la iye amene amandiona silidzandionanso, Maso anu adzandiyang’ana, koma ine kudzakhala kulibe.+   Mtambo umafika kumapeto ake n’kutha. Chimodzimodzi ndi munthu amene wapita ku Manda,* sadzabwerako.+ 10  Sadzabwereranso kunyumba yake, Ndipo anthu a pamalo ake sadzamuzindikiranso.+ 11  Choncho, ine sinditseka pakamwa panga. Ndilankhula chifukwa cha kuvutika mumtima,+ Ndilankhula za nkhawa zanga, chifukwa moyo wanga ukupweteka. 12  Kodi ine ndine nyanja, kapena chilombo cha m’nyanja, Kuti mundiikire mlonda?+ 13  Ndikanena kuti, ‘Bedi langa linditonthoza, Bedi langa lindithandiza kusenza nkhawa zanga,’ 14  Inuyo mumandiopseza ndi maloto, Ndipo mumandichititsa mantha ndi masomphenya. 15  Chotero moyo wanga wasankha kubanika, Wasankha imfa+ m’malo mwa mafupa angawa. 16  Moyo ndaukana,+ sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.* Ndisiyeni chifukwa masiku anga ndi ochepa kwambiri.+ 17  Kodi munthu ndani+ kuti mumulere, Ndi kuti muzimuganizira? 18  Iye ndani kuti muzimuganizira m’mawa uliwonse, Ndi kuti muzimuyesa nthawi zonse?+ 19  N’chifukwa chiyani simukusiya kundiyang’ana,+ Kapena kundisiya kuti ndimezeko malovu? 20  Ngati ndachimwa, ndingakuchiteni chiyani Inu amene mumaonetsetsa anthu?+ N’chifukwa chiyani mwalunjika ine, kuti ndikhale cholemetsa kwa inu? 21  N’chifukwa chiyani simukundikhululukira machimo anga,+ Ndi kunyalanyaza zolakwa zanga? Pakuti tsopano ndigona m’fumbi.+ Mudzandifunafuna koma ine kudzakhala kulibe.”

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 5.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.