Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 38:1-41

38  Tsopano Yehova anamuyankha Yobu kuchokera mumphepo yamkuntho+ kuti:   “Kodi amene akuphimba malangizo anga Ndi mawu ake opanda nzeruyu ndani?+   Takokera chovala chako n’kuchimanga m’chiuno ngati mwamuna wamphamvu. Ndikufuna ndikufunse mafunso ndipo iweyo undiyankhe.+   Kodi unali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi?+ Ndiuze ngati uli womvetsa zinthu.   Ndani anaika miyezo yake, ngati ukudziwa, Kapena ndani anatambasulirapo chingwe choyezera?   Kodi maziko ake anazikidwa pa chiyani?+ Kapena ndani anaika mwala wake wapakona,   Pamene nyenyezi za m’mawa+ zinafuula pamodzi mokondwera, Ndiponso pamene ana onse a Mulungu+ anayamba kufuula ndi chisangalalo?   Ndani anatseka nyanja ndi zitseko,+ Imene inayamba kuyenda ngati kuti ikutumphuka m’mimba?   Pamene ndinaika mtambo ngati chovala chake, Ndi mdima wandiweyani ngati nsalu yoikulungira. 10  Ndipo ndinaiikira lamulo, Ndinaiikiranso mpiringidzo ndi zitseko.+ 11  Kenako ndinaiuza kuti, ‘Ukhoza kufika apa, koma usapitirirepo,+ Ndipo mafunde ako aatali azilekezera pamenepa.’+ 12  Kodi kuyambira masiku ako oyambirira unalamula m’mawa?+ Kodi ndiwe unachititsa m’bandakucha kudziwa malo ake, 13  Kuti kuwala kwake kufike mpaka kumalekezero a dziko lapansi, Kuti anthu oipa asansidwe n’kuchotsedwamo?+ 14  Dzikolo limadzisintha ngati dongo+ pansi pa chodindira, Ndipo zinthu zimakhala pamalo awo ngati kuti zavala zovala. 15  Kuwala kwa oipa kumachotsedwa,+ Ndipo dzanja lokwezedwa m’mwamba limathyoledwa.+ 16  Kodi unafika ku akasupe a nyanja, Kapena kodi unayamba wakafunafunapo madzi akuya?+ 17  Kodi anakuvundukulira zipata za imfa,+ Kapena zipata za mdima wandiweyani,+ kodi ungathe kuziona? 18  Kodi unaganizapo mozama za kukula kwa dziko lapansi?+ Ndiuze ngati ukudziwa zonse. 19  Kodi njira yopita kumene kuwala kumakhala ili kuti?+ Nanga mdima, kwawo n’kuti, 20  Kuti uzipititse kumalire awo, Ndi kuti udziwe njira zopita kunyumba kwawo? 21  Kodi ukudziwa popeza pa nthawiyo unali utabadwa,+ Ndiponso chifukwa chakuti masiku ako ndi ochuluka? 22  Kodi unalowapo munkhokwe ya chipale chofewa,+ Kapena umaziona nkhokwe za matalala,+ 23  Zimene ndazisungira nthawi ya zowawa, Ndi tsiku lomenyana komanso lankhondo?+ 24  Kodi njira imene kuwala kumadzigawira ili kuti, Ndiponso njira imene mphepo ya kum’mawa+ imamwazikira padziko lapansi ili kuti? 25  Ndani anagawa ngalande ya madzi osefukira, Ndi njira ya mtambo wa mvula yamabingu,+ 26  Kuti achititse mvula kugwa padziko pamene palibe munthu,+ Ndi kuchipululu kumene kulibe munthu aliyense, 27  Kuti inyowetse malo owonongeka ndi mvula yamkuntho ndiponso ouma, Komanso kuti imeretse udzu?+ 28  Kodi mvula ili ndi tate wake,+ Kapena ndani anabereka mame?+ 29  Kodi madzi oundana amachokera m’mimba   mwa ndani, Ndipo mame oundana+ a m’mlengalenga anawabereka ndani? 30  Madzi amadzibisa ngati kuti ali pansi pa mwala, Ndipo pamwamba pa madzi akuya pamauma.+ 31  Kodi ungamange zingwe gulu la nyenyezi la Kima, Kapena kodi ungamasule zingwe za gulu la nyenyezi la Kesili?+ 32  Kodi ungatulutse gulu la nyenyezi la Mazaroti pa nthawi yake? Ndipo kodi ungatsogolere gulu la nyenyezi la Asi pamodzi ndi ana ake? 33  Kodi malamulo akuthambo ukuwadziwa,+ Kapena kodi ulamuliro wake ungauike padziko lapansi? 34  Kodi ungafuulire mtambo Kuti madzi ochuluka akukhuthukire?+ 35  Kodi ungauze mphezi kuti zibwere kwa iwe N’kudzakuuza kuti, ‘Ndife pano, tabwera’? 36  Ndani anaika nzeru+ m’mitambo, Kapena zinthu zochitika kuthambo, ndani anazipatsa kuzindikira?+ 37  Ndani amene ali ndi nzeru zoti angathe kudziwa chiwerengero cholondola cha mitambo, Kapena zosungira madzi akumwamba, ndani angathe kuzipendeketsa,+ 38  Fumbi likasanduka matope n’kumayenderera ngati chitsulo chosungunula, Ndiponso zibuma zadothi zikamatana? 39  Kodi mkango ungausakire nyama, Ndipo kodi ungakhutiritse mikango yamphamvu yanjala kwambiri,+ 40  Ikamyata m’malo amene imabisala,+ Kapena ikabisala patchire kuti igwire nyama? 41  Ndani amakonzera khwangwala chakudya,+ Ana ake akamalirira Mulungu kuti awathandize, Akamadzandira chifukwa chosowa chakudya?

Mawu a M'munsi