Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 36:1-33

36  Elihu anapitiriza kunena kuti:   “Ndilezereni mtima kwa kanthawi kochepa ndipo ndikuuzaniKuti mawu alipobe oti ndinene m’malo mwa Mulungu.   Zimene ndinene ndizitenga kutali,Ndipo ndilengeza kuti amene anandipanga, ndiye mwiniwake wa chilungamo.   Chifukwa mawu anga ndithu si onama.Wodziwa bwino zinthu kwambiri ali ndi inu.   Mulungutu ndi wamphamvu+ ndipo sadzakana munthu.Iye ali ndi mphamvu zazikulu zomvetsa zinthu.   Iye sadzasiya woipa aliyense ali wamoyo,+Koma adzapereka chiweruzo cholungama kwa osautsika.+   Sadzachotsa maso ake pa aliyense wolungama.+Adzaika mafumu pamipando yachifumu,+Adzawachititsa kuti alamulire kwamuyaya, ndipo iwo adzakhala ndi mphamvu zambiri.   Anthu akamangidwa m’matangadza,+Amagwidwa ndi zingwe za masautso.   Ndiyeno iye adzawauza za momwe iwo amachitira zinthuNdiponso zolakwa zawo, chifukwa iwo amadzikuza. 10  Iye adzatsegula makutu awo kuti iwo amve pamene iye akuwalimbikitsa,+Ndipo adzawauza kuti asiye kuchita zopweteka ena.+ 11  Akamumvera ndi kumutumikira,Adzamaliza bwino masiku awo,Ndipo adzamaliza zaka zawo mosangalala.+ 12  Koma akapanda kumvera, adzaphedwa+ ndi chida.+Iwo adzafa ali osadziwa. 13  Anthu ampatuko adzaunjika mkwiyo.+Iwo sadzalirira thandizo chifukwa chakuti iye wawamanga. 14  Iwo adzafa ali anyamata,+Ndipo moyo wawo udzathera pakati pa mahule aamuna a pakachisi. 15  Iye adzapulumutsa wozunzika m’masautso ake,Ndipo adzatsegula makutu awo pamene akuponderezedwa. 16  Ndithu iye adzakukopani n’kukuchotsani pakamwa pa zowawa.+M’malomwake padzakhala malo otakasuka,+ osati opanikiza,Ndipo chitonthozo cha patebulo panu chidzakhala chodzaza ndi mafuta.+ 17  Ndithu mudzakhutira woipa+ akadzaweruzidwa.Chiweruzo ndi chilungamo zidzakhazikika. 18  Samalani kuti mkwiyo+ usakuchititseni kuwomba m’manja chifukwa cha njiru,Ndipo dipo lalikulu+ lisakusocheretseni. 19  Kodi kulira kwanu kopempha thandizo kudzakupindulirani?+ Ayi, sikudzakupindulirani ngakhalenso pa mavuto,Ngakhale muyesetse mwamphamvu bwanji.+ 20  Musapumire m’mwamba polakalaka usiku,Pamene anthu amabwera kuchokera kumene anali. 21  Samalani kuti musabwerere ku zinthu zopweteka ena,+Chifukwa mwasankha zimenezi m’malo mwa masautso.+ 22  Mulungutu amachita zinthu zapamwamba ndi mphamvu zake.Kodi mphunzitsi winanso ndani wofanana naye? 23  Ndani wam’funsa kuti afotokoze za njira yake,+Ndipo ndani wamuuza kuti, ‘Mwachita zosalungama’?+ 24  Kumbukirani kuti muyenera kutamanda ntchito zake,+Zimene anthu amaziimba. 25  Anthu onse amaziyang’anitsitsa.Munthu amaziyang’ana ali patali. 26  Mulungu ndi wokwezeka kuposa mmene tikudziwira.+Zaka zake n’zosawerengeka.+ 27  Pakuti iye amakoka madontho a madzi.Madonthowo amasefeka n’kutsika ngati mvula ndi nkhungu, 28  Moti mitambo imakha,Imakhetsa madzi ochuluka pa anthu. 29  Zoonadi, ndani angamvetse mmene mitambo imatambasukira?Komanso kugunda kochokera kumsasa wake? 30  Amaikuta ndi kuwala kwake,+Ndipo waphimba mizu ya nyanja. 31  Ndi zimenezi, iye amaweruza mokomera mitundu ya anthu.Amapereka chakudya chochuluka.+ 32  Iye wafumbata mphezi m’manja mwake,Ndipo amailamula kuti igwere woukira. 33  Kugunda kwake kumanena za iye.Ziwetonso zimanena za amene akubwera.

Mawu a M'munsi