Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 35:1-16

35  Elihu anapitiriza kulankhula kuti:   “Kodi mukuona ngati chimenechi n’chilungamo? Inuyo mwanena kuti, ‘Ndine wolungama kuposa Mulungu.’+   Mwanena kuti, ‘Kodi kulungamako n’kwantchito yanji kwa inu?+ Kodi kundipindulitsa chiyani kuposa chimene ndikanapindula pochimwa?’+   Ineyo ndikuyankhani inuyo Ndi mabwenzi+ anu muli nawowo.   Yang’anani kumwamba+ muone. Muona kuti mitambo+ ili pamwamba kuposa inu.   Mukachimwa, kodi mumapindula chiyani chotsutsana naye?+ Ndipo kupanduka kwanu kukawonjezeka, kodi mumam’chitira chiyani chomuipira?   Ngati ndinudi wosalakwa, kodi mumam’patsa chiyani? Kodi amalandira chiyani kuchokera m’manja mwanu?+   Kuipa kwanu kungapweteke munthu ngati inu nomwe,+ Ndipo chilungamo chanu chingakomere mwana wa munthu wochokera kufumbi.+   Chifukwa cha kuchuluka kwa kuponderezedwa, iwo amangokhalira kufuula popempha thandizo.+ Amangokhalira kulirira thandizo chifukwa cha dzanja la amphamvu.+ 10  Koma palibe wanena kuti, ‘Kodi Mulungu, Wondipanga Wamkulu,+ ali kuti, Amene amapatsa anthu nyimbo usiku?’+ 11  Iye ndiye amatiphunzitsa+ zambiri kuposa nyama zakutchire,+ Ndipo amatipatsa nzeru kuposa ngakhale zolengedwa zouluka m’mlengalenga. 12  Iwo amangokhalira kulirira thandizo, koma iye sawayankha+ Chifukwa cha kunyada+ kwa anthu oipa. 13  Koma Mulungu samva kufuula kwa anthu olankhula zinthu zonama,+ Ndipo Wamphamvuyonse sawaona.+ 14  Nanga kuli bwanji mukanena kuti simumuona?+ Mlanduwo uli pamaso pake, choncho muzimuyembekezera ndi nkhawa.+ 15  Tsopano popeza sanakulangeni chifukwa cha mkwiyo wake,+ Iye sanaonenso kupupuluma kwanu.+ 16  Yobu akatsegula pakamwa pake amalankhula zopanda pake. Amachulukitsa mawu osonyeza kuti palibe chimene akudziwa.”+

Mawu a M'munsi