Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 34:1-37

34  Elihu anapitiriza kulankhula kuti:   “Mvetserani mawu anga, anthu anzeru inu.Ndipo anthu odziwa zinthu inu, ndimvereni.   Pakuti khutu limasiyanitsa mawu,+Monga mmene m’kamwa mumasiyanitsira kakomedwe ka chakudya.+   Tiyeni tidzisankhire chiweruzo.Tidziwe tokha pakati pathu chimene chili chabwino.   Pakuti Yobu wanena kuti, ‘Ndithu ine si ine wolakwa,+Koma Mulungu wapotoza chiweruzo changa.+   Kodi ndikunama za mmene chiweruzo changa chiyenera kukhalira?Chilonda changa chachikulu sichikupola ngakhale kuti sindinachimwe.’+   Kodi ndi mwamuna wamphamvu uti amene ali ngati Yobu,+Yemwe amamwa mnyozo ngati madzi?+   Iye ndithu ali pa ulendo wokachita ubwenzi ndi anthu ochita zopweteka ena,Komanso ali pa ulendo wokayenda ndi anthu oipa.+   Chifukwa wanena kuti, ‘Mwamuna wamphamvu sapindula kanthu+Akamachita zosangalatsa Mulungu.’ 10  Choncho inu amuna a mtima+ womvetsa zinthu, ndimvereni.Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe,Ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono. 11  Pakuti iye amapereka mphoto kwa munthu wochokera kufumbi malinga ndi zochita zake,Ndipo amam’bweretsera zinthu zogwirizana ndi njira yake. 12  Ndithudi, Mulungu sachita zoipa,+Ndipo Wamphamvuyonse sakhotetsa chilungamo.+ 13  Ndani wam’patsa dziko lapansi?Ndipo ndani wam’patsa ulamuliro panthaka yonse? 14  Akaika mtima wake pa munthu aliyense,Akatenga mzimu* ndi mpweya wa munthuyo,+ 15  Zamoyo zonse zimafera limodzi,Ndipo munthu amabwerera kufumbi. 16  Choncho ngati mumamvetsa zinthu, mvetserani izi.Mvetserani mawu anga. 17  Kodi zoonadi munthu wodana ndi chilungamo angalamulire?Ngati munthu wamphamvu ali wolungama, kodi munganene kuti ndi woipa? 18  Kodi munthu anganene kwa mfumu kuti, ‘Ndinu wopanda pake’?Kapena angauze anthu olemekezeka kuti, ‘Ndinu oipa’? 19  Alipo amene sanakonderepo akalonga,Ndipo saganizira kwambiri wolemekezeka kuposa wonyozeka,Chifukwa onsewo anapangidwa ndi manja ake.+ 20  Iwo amafa mwadzidzidzi,+ ngakhale pakati pa usiku.Anthuwo amagwedezeka uku ndi uku n’kufa,Ndipo amphamvu amachoka popanda dzanja lowachotsa. 21  Pakuti maso ake amayang’anitsitsa njira za munthu,Ndipo amaona mayendedwe ake onse. 22  Kulibe mdima wandiweyaniWoti amene akuchita zopweteka ena abisaleko.+ 23  Pakuti iye saikiratu nthawi yoti munthu aliyenseApite kukaweruzidwa ndi Mulungu. 24  Iye amaphwanya amphamvu+ popanda kuwafufuza,Ndipo amachititsa ena kuima m’malo mwawo.+ 25  Chotero iye amazindikira ntchito zawo.+Amawagwetsa usiku ndipo iwo amatswanyidwa. 26  Amawamenya monga oipa,Pamalo pomwe ena akuonerera. 27  Chifukwa asiya kumutsatira,Ndipo sasamala za njira zake zonse,+ 28  Kuti achititse kulira kwa wonyozeka kupita kwa iye.Choncho iye amamva kulira kwa osautsika. 29  Iye akachititsa bata, ndani angamudzudzule?Ndipo akabisa nkhope yake,+ ndani angamuone?Kaya abisire nkhope yake mtundu+ kapena munthu, n’chimodzimodzi. 30  Kuti munthu wopanduka asalamulire,+Ndi kuti pasakhale misampha ya anthu. 31  Kodi munthu ndithu anganene kwa Mulungu kuti,‘Ndapirira ngakhale kuti sindinachite cholakwa?+ 32  Ngakhale kuti sindikuona chilichonse, inuyo ndiphunzitseni?Ngati ndachita chosalungama chilichonse,Sindidzachichitanso?’+ 33  Kodi iye angakulipire mogwirizana ndi mmene ukuganizira, chifukwa chakuti ukukana chiweruzo chake?Chifukwa chakuti iweyo wasankha wekha, osati ine?Tsopano nena zimene ukudziwa. 34  Anthu a mtima womvetsa zinthu+ adzandiuza,Ngakhale munthu wanzeru komanso wamphamvu amene akundimvetsera adzandiuza kuti, 35  ‘Yobu sadziwa zimene akunena,+Ndipo amanena mawu osonyeza kuti iye ndi wosazindikira.’ 36  Atate anga, Yobu ayesedwe mpaka pamapetoChifukwa cha zimene anali kuyankha pakati pa amuna ochita zopweteka anzawo.+ 37  Chifukwa pa tchimo lake akuwonjezerapo kupanduka.+Akuwomba m’manja pakati pathu ndipo akuchulutsa zonena zake zotsutsana ndi Mulungu woona.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 4.